bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Jonah 4
Jonah 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
1
Chifukwa cha zimenezi Yona adakhumudwa kwambiri, nakwiya.
2
Tsono adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, nzimenezitu zimene ndinkaopa ndili kwathu. Nchifukwa chake ndidaayesetsa kuthaŵira ku Tarisisi. Ndidaadziŵa kuti Inu ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, woleza mtima ndi wa chikondi chosasinthika, ndiponso wokhululukira machimo nthaŵi zonse.
3
Ndiye tsono Inu Chauta, ndapota nanu, ingondiphani basi. Nkhwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.”
4
Chauta adamufunsa kuti, “Kodi iwe wachita bwino pokwiya chotere?”
5
Yona adatuluka mumzindamo nakakhala pansi chakuvuma kwake. Kumeneko adadzimangira chithando nakhala m'menemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitike mumzindamo.
6
Tsono Chauta Mulungu adameretsa msatsi kuti uchitire Yona mthunzi ndi kumchotsa mavuto ake. Yona adakondwa kwambiri chifukwa cha msatsiwo.
7
Koma m'maŵa mwake mbandakucha, Mulungu adatuma mphanzi kuti ikadye msatsiwo, ndipo udafota.
8
Pamene dzuŵa linkatuluka, Chauta adautsira Yona mphepo yotentha kuti iwombe kuchokera kuvuma. Dzuŵa lidamtentha pa mutu Yona, mpaka kulenguka nalo. Tsono adapempha kuti afe, adati, “Nkwabwino kuti ndife kupambana kukhala moyo.”
9
Koma Mulungu adamufunsa kuti, “Kodi wachita bwino pokwiya chifukwa cha msatsiwu?” Iye adati, “Inde ndachita bwino kukwiya. Kukwiya kwake nkofa nako.”
10
Chauta adati, “Iwe ukumvera chisoni msatsi umene sudaugwirire ntchito, sindiwe udaubzala ndi kuukuza. Udamera pa usiku umodzi, nufanso pa usiku umodzi.
11
Nanga Ine, kodi sindiyenera kuumvera chisoni mzinda waukulu wa Ninive? M'mene mujatu muli anthu opitirira zikwi 120, amene sadziŵa kusiyanitsa kuti zabwino nziti, zoipa nziti, mulinso ziŵeto zochuluka.”
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
All chapters:
1
2
3
4