bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nahum 1
Nahum 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Uwu ndi uthenga wonena za mzinda wa Ninive. Uthengawu ukufotokoza za zimene Nahumu wa ku Elikosi adaziwona m'masomphenya.
2
Chauta ndi Mulungu wansanje ndiponso wolipsira. Chauta amalanga, ndipo ndi wamkali. Chauta amalipsira amaliwongo ake amakwiyira adani ake.
3
Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
4
Akangoilamula nyanja, imauma, amaumitsanso mitsinje yonse. Zomera za ku Basani ndi za ku Karimele zimauma, maluŵa a ku Lebanoni amafota.
5
Mapiri amagwedezeka pamaso pake, magomo amasungunuka. Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake, ndiye kuti dziko ndi zonse zokhala m'menemo.
6
Kodi ndani angathe kuima pamaso pa Chauta, Iye atakwiya? Kodi ndani angathe kupirira ukali wake? Ukali wake umayaka ngati moto, matanthwe amadyukuka pamaso pake.
7
Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.
8
Koma ndi madzi achigumula adzaononga adani ake, ndipo adzaŵapirikitsira ku malo amdima.
9
Kodi mukukonzekera kumchita Chauta chiwembu chotani? Adzakuwonongani kotheratu. Sadzalira kuŵalipsira kaŵiri adani akewo.
10
Adzaŵatentha kotheratu ngati ziyangoyango za minga ndiponso ngati ziputu zouma.
11
Ku Ninive kudachokera munthu wa cholinga choipa, wofuna kuchita Chauta chiwembu.
12
Zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, “Ngakhale Aasiriyawo ndi amphamvu ndiponso ndi ambiri, adzaonongeka ndi kutheratu. Koma inu anthu anga, ngakhale ndidakulangani, sindidzakulanganinso.
13
Tsopano ndidzathyola goli limene adakuikani m'khosi, ndipo ndidzadula maunyolo anu.”
14
Za inu a ku Ninive Chauta walamula kuti, “Simudzakhala ndi adzukulu otchedwa dzina lanu. Ndidzaononga mafano osema ndi oumba m'nyumba ya milungu yanu. Ndidzakukumbirani manda, chifukwa ndinu opandapake.”
15
Ona, kumapiri kukubwera munthu, iyeyu ali ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere. Inu a ku Yuda muzisunga masiku achikondwerero; zimene mudalumbira, muzizichitadi. Anthu oipawo sadzakuthiraninso nkhondo. Adaonongeka kotheratu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3