bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nahum 2
Nahum 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Inu a ku Ninive, othira nkhondo akubwera kudzakuwonongani. Ikani ankhondo pa malinga! Muziyang'ana ku mseu! Konzekerani nkhondo! Valani dzilimbe!
2
Patsala pang'ono kuti Chauta abwezere ulemerero wa Israele, monga udaaliri kale, ofunkha asanalande zinthu zonse ndi kuwononga mphesa zao.
3
Zishango za ankhondo ao nzofiira, asilikali ao onse avala zovala zamlangali. Atandanda pa mizere yankhondo, magaleta ao akuchezimira ngati malaŵi a moto. Akavalo akungoti jodojodo.
4
Magaleta akuthamanga m'miseu. Ali piringupiringu m'mabwalo. Ali ŵaliŵali ngati miyuni yoyaka. Ali ng'aning'ani ngati mphezi.
5
Atsogoleri a ankhondo akuitanidwa, akubwera naphunthwa. Akuthamangira ku linga la mzinda, akuimika chipupa chodzitetezera.
6
Akutsekula zipata zotchinga dziŵe la madzi, kunyumba kwa mfumu kwadzaza mantha.
7
Mfumukazi yake yatengedwa ukapolo. Adzakazi ake akulira ngati nkhunda, ndipo akudzigunda pa chifuwa.
8
Ninive wasanduka ngati chidziŵe, chimene madzi ake ali faa kutuluka. Ena akufuula kuti, “Imani! Imani!” Koma palibe amene akubwerera.
9
Funkhani siliva! Funkhani golide! Chuma chake nchosatha, za mtengo wapatali nzosaŵerengeka.
10
Mzinda wa Ninive waonongeka, wasanduka bwinja, wopanda anthu. Mitima yachokamo, maondo akuwombana, m'nkhongono muli zii, nkhope zasinthika ndi mantha.
11
Kodi tsopano mzinda uja uli kuti? Unali ngati phanga la mikango, m'mene ana ake ankadyeramo, m'mene mikango yonse inkakhala mopanda mantha.
12
Mkango wamphongo unkapha nyama yokwanira mkango waukazi ndi ana ake. Unkadzaza phanga lakelo ndi nyama yokadzulakadzula.
13
Chauta Wamphamvuzonse akuuza a ku Ninive kuti, “Ine sindikugwirizana nanu, ndidzakutentherani magaleta anu. Lupanga lidzakuwonongerani ankhondo anu amene ali ngati mikango. Ndidzakulandani zonse zimene mudafunkha pa dziko lapansi. Amithenga anu sadzamvekanso mau.”
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3