bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Nahum 3
Nahum 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
1
Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi a anthu ambiri, mzinda wodzaza ndi mabodza ndi zakuba, wokonda kufunkha mosalekeza.
2
Imvani kulira kwa zikoti, kukokoma kwa mikombero, likitilikiti wa akavalo ndi kulilima kwa magaleta.
3
Okwera pa akavalo akuthamanga, malupanga ali ŵaliŵali, mikondo ili phuliphuli. Afa anthu ambiri, mitembo yati vuu, yosaŵerengeka, anthu kumaphunthwa pa mitemboyo.
4
Zonsezo zachitika chifukwa cha zonyansa zochuluka za Ninive, mkazi wachiwerewere uja. Ankakopa anthu ndi kukongola kwake konyenga. Ankanyengadi anthu a mitundu yonse ndi zadama zake nakopa mafuko ndi zithumwa zake.
5
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ine sindikugwirizana nawe, ndidzakuvula ndi kukunyazitsa. Anthu a mitundu yonse adzaona maliseche ako, udzachita manyazi pamaso pa maiko onse.
6
Ndidzakuthira zonyansa, ndidzakunyodola, ndipo ndidzakusandutsa chinthu chomachiseka.
7
Ndipo onse okuwona adzakuthaŵa, adzati, ‘Ninive wasanduka bwinja, adzamlira ndani?’ Ndidzamtenga kuti woti akusangalatse?” Akuterotu Chauta.
8
Kodi iwe Ninive ndiwe wopambana Thebesi? Suja mzinda umenewu unali m'mbali mwa mtsinje wa Nailo utazingidwa ndi madzi. Madziwo anali ngati khoma lake ndi linga lake?
9
Mzindawo unkalamulira Etiopiya ndi Ejipito, mphamvu zake zinali zopanda malire. Aputi ndi Alibiya ndiwo ankagwirizana nawo.
10
Komabe anthu a ku Thebesi adagwidwa, adasanduka akapolo. Ana ao adaŵakankhanthitsa pansi m'miseu yonse ya mumzindamo. Adani adagaŵana anthu otchukawo mwamaere. Akuluakulu onse adaŵamanga ndi maunyolo.
11
Iwenso Ninive udzachita ngati waledzera, mutu wako udzazungulira. Nawenso udzafunafuna malo othaŵirako.
12
Malinga ako onse adzakhala ngati mitengo ya nkhuyu zoyamba kupsa. Akaigwedeza, nkhuyuzo zimagwera m'kamwa mwa wofuna kuzidya.
13
Ankhondo ako ali ngati akazi. Zipata za dziko lako zaŵatsekukira adani ako, ndipo moto wapsereza mipiringidzo yake.
14
Mutungiretu madzi kuti adzakwanire pa nthaŵi yokuzingani, limbitsani malinga anu. Pondani dothi, ponyani m'chikombole, ndipo muumbe njerwa.
15
Ngakhale mutero, moto udzakupserezanibe, ndipo lupanga lidzakukanthani, mudzapululuka ngati dzombe. Swanani ngati dzombe, chulukanani ngati ziwala.
16
Mudachulukitsa anthu anu amalonda kupambana nyenyezi zamumlengalenga. Koma onsewo adamwazikana ngati dzombe.
17
Nduna zanu zili ngati dzombe. Akuluakulu anu ali ngati ziwala, zimene zimangokangamira pa khoma kukazizira. Koma dzuŵa likamatuluka, zimauluka, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene amadziŵa kumene zapita.
18
Iwe mfumu ya Aasiriya, nduna zako zaferatu. Akuluakulu ako apitiratu. Anthu ako amwazikira ku mapiri, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe woŵasonkhanitsa.
19
Palibe mankhwala a bala lako, chilonda chako sichingapole. Onse amene amamva za iwe, amaomba m'manja mokondwa. Kodi alipo wina amene sadazilaŵepo nkhanza zako zosathazi?
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
All chapters:
1
2
3