bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zephaniah 1
Zephaniah 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
1
Pa nthaŵi ya Yosiya, mwana wa Amoni, mfumu ya ku Yuda, Chauta adamupatsa uthenga Zefaniya, mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya.
2
Chauta adati, “Ndidzafafaniziratu zonse za pa dziko lapansi.”
3
“Ndidzafafaniziratu anthu ndi nyama zomwe. Ndidzaononga mbalame zamumlengalenga ndi nsomba zam'nyanja. Ndidzagwetsa anthu ochimwa. Ndidzafafaniziratu mtundu wa anthu kuti usaonekenso pa dziko lapansi,” akuterotu Chauta.
4
“Ndidzasamula dzanja langa kuti ndilange anthu a m'dera la Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu. Ndidzafafaniziratu zotsalira zonse za Baala pa malo ano. Palibe aliyense amene adzakumbukirenso ansembe a fanolo.
5
Ndidzafafanizanso amene amaŵerama pa madenga ao nkumapembedza dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi. Ndidzaononganso amene amati kwinaku akulambira Chauta ndi kulumbira m'dzina lake, kwinaku nkumalumbira m'dzina la Milikomu.
6
Iwowo adafulatira Chauta osamtsatanso, safuna kupembedza Chauta, kapena kumpempha nzeru.”
7
Khalani chete pamaso pa Ambuye Chauta! Tsikutu la Chauta layandikira. Chauta wakonza kuti anthu ake adzaperekedwe ngati nsembe, ndipo wapatuliratu oitanidwa odzapereka nsembeyo.
8
Chauta akuti, “Pa tsiku limenelo la nsembe yanga ndidzalanga ana a mfumu ndi akalonga ake, ndi onse otengera zachilendo.
9
Pa tsiku limenelo ndidzalanga onse olumpha pa chiwundo, ndiponso amene amachita zankhanza ndi zonyenga zambiri.”
10
Chauta akunena kuti, “Pa tsiku limenelo kulira kwakukulu kudzamveka ku Chipata cha Msika wa Nsomba; kulira kwakukuluko kudzamveka ku chigawo cham'kati cha mzinda wa Yerusalemu; kudzamvekanso kugunda kuchokera ku mapiri.
11
Inu okhala ku chigwa cha mzinda lirani komvetsa chisoni, chifukwa amalonda onse atha, onse ogulitsa siliva aonongeka.
12
Pa nthaŵi imeneyo ndidzafufuzafufuza mu Yerusalemu ndi nyale, ndipo ndidzaŵalanga anthu ongokhala khale ngati vinyo wosakhutchumula, amene mumtima mwao amati, ‘Chauta sadzachitapo chabwino, kapena kuchitapo choipa.’
13
Anthu otereŵa chuma chao adani adzachifunkha, nyumba zao adzaziphwasula. Adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo. Adzabzala mphesa, koma sadzamwa vinyo wake.”
14
Tsiku lalikulu la Chauta lili pafupi, layandikira ndipo likudza mofulumira. Tsikulo kubwera kwake nkopweteka, ngakhale ankhondo amphamvu omwe akulira pamenepo.
15
Tsikulo lidzakhala tsiku la mkwiyo wa Chauta, tsiku la mavuto ndi mazunzo, tsiku la kuwonongeka ndi kupasuka kwa zinthu, tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi labii kuda.
16
Tsiku limenelo kudzamveka lipenga ndi kufuula kwankhondo, kwa asilikali othira nkhondo mizinda ya malinga ndiponso nsanja zankhondo za Yerusalemu.
17
Chauta akuti, “Chifukwa anthuwo adandichimwira, ndidzaŵasautsa koopsa, kotero kuti azidzayenda ngati akhungu. Magazi ao adzachita kuti mwaa ngati fumbi, matupi adzangoti vuu, nkumaola ngati ndoŵe.
18
Ngakhale siliva wao kapena golide wao sadzatha kuŵaombola, tsiku la mkwiyo wa Chautalo. Ukali wake wotentha ngati moto, udzapsereza dziko lonse, ndipo mwadzidzidzi adzathetsa onse okhala m'menemo.”
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3