bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zephaniah 2
Zephaniah 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
1
Inu anthu opanda manyazinu, chitani msonkhano, mulape,
2
adani asanakumwazeni ngati mungu, ukali woopsa wa Chauta usanakugwereni, tsiku la mkwiyo wa Chauta lisanakupezeni.
3
Funafunani Chauta, inu nonse odzichepetsa, inu amene mumamvera malamulo ake. Chitani zolungama, khalani odzichepetsa. Mwina mwake mudzatha kupulumuka pa tsiku la mkwiyo wa Chauta.
4
Mzinda wa Gaza udzasiyidwa, Asikeloni adzasanduka bwinja. Anthu a ku Asidodi adzapirikitsidwa masana mwadzidzidzi, Akeroni adzapasuka.
5
Tsoka kwa inu okhala m'mbali mwa nyanja, inu mtundu wa Akeretinu Mau a Chauta akukudzudzulani, inu anthu a ku Kanani, dziko la Afilisti, akuti, “Ndidzakuwonongani nonse sipadzatsala ndi mmodzi yemwe.”
6
Dziko limene lili m'mphepete mwa nyanja, lidzasanduka madambo a abusa, ndi makola a nkhosa.
7
Kumeneko kudzakhala dziko la otsala a m'banja la Yuda. Azidzadyetsa nkhosa zao m'mbali mwanyanjamo, ndipo madzulo azidzagona ku nyumba za ku Asikeloni. Pakuti Chauta, Mulungu wao adzaŵasamalira, ndiye amene adzaŵabwezere ufulu wao.
8
Chauta akuti, “Ndamva kunyoza kwa Amowabu, ndiponso kutukwana kwa Aamoni, m'mene anyozera anthu anga ndi m'mene adzikuzira m'dziko mwao.
9
Nchifukwa chake Ine Chauta Wamphamvuzonse ndikulumbira kuti, Pali Ine ndemwe, Mulungu wamoyo wa Israele, Amowabu adzaonongedwa ngati anthu a ku Sodomu, Aamoni adzaonongedwa ngati anthu a ku Gomora. Malowo adzakhala ngati dera la zitsamba za khwisa ndi la nkhuti za mchere, dziko lachipululu mpaka muyaya. Otsala mwa anthu anga adzafunkha malowo. Opulumuka a mtundu wanga adzalandira malowo ngati dziko lao.”
10
Chimenechi chidzakhala chilango choyenerera kunyada kwaoko, chifukwa adanyoza anthu a Chauta Wamphamvuzonse.
11
Motero Chauta adzaŵaopsa kwambiri. Adzaononga milungu yonse ya pa dziko lapansi. Mitundu yonse ya anthu idzampembedza Chauta, mtundu uliwonse ku dziko lakwao.
12
Inunso Aetiopiya, Chauta adzakukanthani ndi lupanga lake.
13
Chauta adzasamulira dzanja lake kumpoto ndi kuwononga dziko la Asiriya. Mzinda wa Ninive adzausandutsa bwinja, udzakhala wagwaa ngati chipululu.
14
Choncho zoŵeta zizidzagona kumeneko chimodzimodzinso nyama zonse zakuthengo. Adembo ndi akanungu azidzagona pa makapotolosi ake. Akadzidzi azidzalira pa windo, ndipo makwangwala azidzakhala pa bwalo lake. Mitengo yake yamkungudza adzaisadza.
15
Umenewo ndiwo mzinda umene unkadzimva kuti ndi wokhazikika, umene mumtima mwake unkati, “Ine pano! Palibenso wina ai!” Tauwonani m'mene wasakazikira tsopano! Wasanduka bwinja lokhalamo nyama zakuthengo. Aliyense wodutsamo azidzangotsonya nkumapukusa mutu.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3