bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Zephaniah 3
Zephaniah 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
1
Tsoka kwa Yerusalemu, mzinda wopanduka, wonyansa ndi wankhanza.
2
Sudamvere mau ouchenjeza. Sudasamale mau oudzudzula. Sudakhulupirire Chauta kapena kuyandikira kwa Mulungu wake.
3
Nduna zake zinkakhuluma m'kati mwake, ngati mikango yobangula. Oweruza ake anali ngati mimbulu yoyenda madzulo, yosasiyako ndi fupa lomwe kuti lifike mpaka m'maŵa.
4
Aneneri ake anali achabechabe, anthu osakhulupirika.
5
Koma Chauta ndi wolungama mumzindamo, Iyeyo salakwa. Amaweruza molungama tsiku ndi tsiku, nthaŵi zonse salephera, koma osalungama akuchitabe zoipa opanda manyazi.
6
Chauta akuti, “Ndaononga mitundu yonse ya anthu ndipo malinga ao onse ankhondo ndaŵaphwasula. Miseu yao ndaifafaniza palibenso anthu oyendamo. Mizinda yao yachitika bwinja, mulibe munthu ndi mmodzi yemwe wotsalamo.
7
Ndidaaganiza kuti ndithudi anthu anga andiwopa, kuti avomera malango anga, ndipo kuti saiŵala malamulo anga. Koma ndi pamene iwo adanyanyira kumachita zoipa pa zochita zao zonse.”
8
Chauta akunena kuti, “Nchifukwa chake mundidikire, mudikire tsiku limene ndidzakuimbeni mlandu. Pakuti ndatsimikiza zosonkhanitsa mitundu ya anthu pamodzi ndi maufumu onse, kuti ndiŵaonetse kusakondwa kwanga amve ululu wa ukali wanga. Dziko lonse lapansi lidzapserera ndi moto waukali wa mkwiyo wanga.”
9
“Pamenepo ndidzasintha malankhulidwe a mitundu yonse, nkuŵapatsa malankhulidwe abwino, kuti onse azitama dzina la Chauta mopemba ndi kumamtumikira mogwirizana.
10
Ngakhale kutali kutsidya kwa mitsinje ya ku Etiopiya, anthu ondipembedza, anthu anga obalalika, adzapereka nsembe kwa Ine.”
11
“Tsiku limenelo inu a ku Yerusalemu simudzachitanso manyazi, chifukwa cha zoipa zonse zimene mudandichita, zimene mudandipandukira nazo. Pakuti nthaŵi imeneyo ndidzakuchotserani onse odzikuza ndi onyada. Simudzachitanso zonyada zanuzo pa phiri langa loyera.
12
Pakati panu ndidzasiya anthu odzichepetsa ndi otsika. Iwowo adzafunafuna populumukira m'dzina la Chauta.
13
Otsala a mu Israeleŵa sadzalakwanso, sadzalankhulanso zabodza, sadzachitanso zonyenga, Adzakhala pabwino mwamtendere, popanda wina woŵaopsa.”
14
Imbani mokweza, inu anthu a ku Ziyoni! Fuulani inu Aisraele! Sangalalani, kondwani ndi mtima wonse, inu okhala mu Yerusalemu.
15
Chauta wachotsa chilango chanu. Wapirikitsa adani anu. Chauta, Mfumu ya Israele, ali nanu pamodzi. Simudzaopanso choipa chilichonse.
16
Tsiku limenelo adzauza Yerusalemu kuti, “Usaope, iwe Ziyoni, usataye mtima.
17
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
18
Monga pa masiku achikondwerero, ndidzakuchotsera tsoka, limene lingokuvutitsa ndi kukunyozetsa.
19
Nthaŵi imeneyo ndidzaŵakhaulitsa onse amene amakuzunzani. Ndidzapulumutsa otayika ndi kusonkhanitsa onse obalalika. Ndidzaŵatamanda ndi kuŵapatsa ulemu, kulikonse kumene adani ao ankaŵachititsa manyazi.
20
Nthaŵi imeneyo ndidzakusonkhanitsani, Ndidzakubwezerani kwanu. Ndidzakusandutsani otchuka ndi olemekezeka, pakati pa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Ndidzakubwezerani ufulu wanu inu mukupenya. Ndatero Ine Chauta.”
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
All chapters:
1
2
3