bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Chronicles 1
2 Chronicles 1
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
1
NDIPO Solomo mwana wa Davide analimbikitsidwa m'ufumu wace, ndipo Yehova Mulungu wace anali naye, namkuza kwakukuru.
2
Ndipo Solomo analankhula ndi Aisrayeli onse, ndi akuru a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga ali yense wa Israyeli, akuru a nyumba za makolo.
3
Ndipo Solomo ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibeoni; pakuti kumeneko kunali cihema cokomanako ca Mulungu adacimanga Mose mtumiki wa Yehova m'cipululu.
4
Koma likasa la Mulungu Davide adakwera nalo kucokera ku Kiriyati Yearimu kumka kumene Davide adalikonzeratu malo; pakuti adaliutsiratu hema ku Yerusalemu.
5
Guwa la nsembe lomwe lamkuwa, adalipanga Bezaleli mwana wa Uri mwana wa Huri linali komweko, ku khomo la kacisi wa Yehova; ndipo Solomo ndi khamulo anafunako.
6
Nakwerako Solomo ku guwa la nsembe pamaso pa Yehova linali ku cihema cokomanako, napereka pamenepo nsembe zopsereza cikwi cimodzi.
7
Usiku womwewo Mulungu anaonekera kwa Solomo, nati kwa iye, Pempha comwe ndikupatse.
8
Nati Solomo kwa Mulungu, Mwacitira Davide atate wanga zokoma zambiri, ndipo mwandiika mfumu m'malo mwace.
9
Tsopano, Yehova Mulungu, likhazikike lonjezano lanu la kwa Davide atate wanga; pakuti mwandiika mfumu ya anthu akucuruka ngati pfumbi lapansi.
10
Mundipatse tsono nzeru ndi cidziwitso, kuti ndituruke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?
11
Ndipo Mulungu anati kwa Solomo, Popeza cinali mumtima mwako ici, osapempha cuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi cidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao,
12
nzeru ndi cidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso cuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhala nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.
13
Momwemo Solomo anadza ku Yerusalemu kucokera ku msanje uli ku Gibeoni, ku khomo la cihema cokomanako; ndipo anacita ufumu pa Israyeli.
14
Ndipo Solomo anasonkhanitsa magareta ndi apakavalo, nakhala nao magareta cikwi cimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi ndi ziwiri; nawaika m'midzi ya magareta ndi kwa mfumu ku Yerusalemu.
15
Ndipo mfumu inatero kuti siliva ndi golidi zikhale m'Yerusalemu ngati miyala, ndi kuti mikungudza icuruke ngati mikuyu yokhala kucidikha.
16
Ndi akavalo amene Solomo anali nao anafuma ku Aigupto; amalonda a mfumu anawalandira magulu magulu, gulu liri lonse mtengo wace.
17
Ndipo anatenga naturuka nalo gareta ku Aigupto mtengo wace masekeli a siliva mazana asanu ndi limodzi, ndi kavalo mtengo wace zana limodzi mphambu makumi asanu; momwemo anawaturutsira mafumu onse a Ahiti, ndi mafumu a Aramu, ndi dzanja lao.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36