bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Chronicles 14
2 Chronicles 14
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 15 →
1
Momwemo Abiya anagona ndi makolo ace, ndipo anamuika m'mudzi wa Davide; ndi Asa mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace, m'masiku ace dziko linaona bata zaka khumi.
2
Ndipo Asa anacita cokoma ndi coyenera m'maso mwa Yehova Mulungu wace,
3
nacotsa maguwa a nsembe acilendo, ndi misanje; naphwanya zoimiritsa zao, nalikha zifanizo zao,
4
nauza Yuda afune Yehova Mulungu wa makolo ao, ndi kucita cilamulo ndi cowauza, Iye.
5
Anacotsanso m'midzi yonse ya Yuda misanje, ndi zifanizo za dzuwa; ndi ufumuwo unacita bata pamaso pace.
6
Ndipo anamanga midzi yamalinga m'Yuda; pakuti dziko linacita bata, analibe nkhondo iyeyu zaka zija, popeza Yehova anampumulitsa.
7
Ndipo anati kwa Yuda, Timange midzi iyi ndi kuizingira malinga, ndi nsanja, zitseko, ndi mipiringidzo; dziko likali pamaso pathu, popeza tafuna Yehova Mulungu wathu; tamfuna Iye, natipatsa mpumulo pozungulira ponse. Momwemo anamanga mosabvutika.
8
Ndipo Asa anali nao ankhondo ogwira zikopa ndi mikondo, a m'Yuda zikwi mazana atatu; ndi a m'Benjamini ogwira malihawo ndi okoka mauta zikwi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu; onsewo ngwazi zamphamvu.
9
Ndipo anawaturukira Zera Mkusi ndi ankhondo zikwi cikwi cimodzi, ndi magareta mazana atatu; nafika iye ku Maresa.
10
Naturuka Asa pamaso pace, nanika nkhondoyi m'cigwa ca Sefata ku Maresa.
11
Ndipo Asa anapfuulira kwa Yehova Mulungu wace, nati, Yehova, palibe wina ngati Inu, kuthandiza pakati pa wamphamvu ndi iye wopanda mphamvu; tithandizeni Yehova Mulungu wathu, titama Inu, taturukira aunyinji awa m'dzina lanu. Yehova, Inu ndinu Mulungu wathu, munthu asakulakeni.
12
Ndipo Yehova anakantha Akusi pamaso pa Asa ndi Yuda, nathawa Akusi.
13
Ndi Asa ndi anthu anali naye anawalondola mpaka ku Gerari, nagwa Akusi ambiri osalimbikanso mphamvu iwowa; pakuti anathyoledwa pamaso pa Yehova ndi ankhondo ace; ndipo anatenga zofunkha zambiri.
14
Ndipo anakantha midzi yonse pozungulira pace pa Gerari; a pakuti mantha ocokera kwa Yehova anawagwera; ndipo anafunkha m'midzi monse, pakuti mudacuruka zofunkha m'menemo.
15
Anakanthanso a m'mahema a ng'ombe, nalanda nkhosa zocuruka, ndi ngamila; nabwerera kumka ku Yerusalemu.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
Recommended Reading
Commentary
2 Chronicles Commentaries
→
Devotional
2 Chronicles Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→