bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Chronicles 22
2 Chronicles 22
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 23 →
1
Ndipo okhala m'Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wace wamng'ono akhale mfumu m'malo mwace; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kucigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda.
2
Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu caka cimodzi; ndi dzina la mace ndiye Ataliya mwana wa Omri.
3
Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi mace acite coipa,
4
Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wace; ndi kuonongeka kwace nkumeneko.
5
Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israyeli, kukayambana nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Gileadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.
6
Nabwerera iye kuti amcize ku Yezreeli, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaeli mfumu ya Aramu, Ndipo Azariya mwana wa Yehoramu mfumu yaYuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu m'Yezreeli, popeza anadwala.
7
Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehocamu; pakuti atafika anaturukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimsi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.
8
Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Israyeli, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.
9
Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala m'Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wace wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.
10
Pamene Ataliya anaona kuti mwana wace adafa, anauka, naononga mbeu yonse yacifumu ya nyumba ya Yuda.
11
Koma Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yoasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wace m'cipinda cogonamo. Momwemo Yehosafati mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wace wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.
12
Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi cimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36