bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
2 Chronicles 33
2 Chronicles 33
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
1
Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi asanu mphambu zisanu.
2
Nacita coipa pamaso pa Yehova, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawacotsa m'dziko mwao pamaso pa ana a Israyeli.
3
Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wace, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.
4
Namanga maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova, imene Yehova adati, M'Yerusalemu mudzakhala dzina langa ku nthawi zonse.
5
Namangiranso khamu lonse la kuthambo maguwa a nsembe m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehoya.
6
Anapititsanso ana ace pamoto m'cigwa ca ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nacita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anacita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wace.
7
Ndipo anaika cifanizo cosema ca fanolo adacipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomo mwana wace, M'nyumba muno ndi m'Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israyeli ndidzaika dzina langa ku nthawi zonse;
8
ndipo sindidzasunthanso phazi la Israyeli ku dziko ndaliikira makolo anu; pokhapo asamalire kucita zonse ndawalamulira, cilamulo conse, ndi malemba, ndi maweruzo, mwa dzanja la Mose.
9
Koma Manase analakwitsa Yuda ndi okhala m'Yerusalemu, kotero kuti anacita coipa koposa amitundu, amene Yehova anawaononga pamaso pa ana a Israyeli.
10
Ndipo Yehova analankhula ndi Manase ndi anthu ace, koma sanasamalira.
11
Motero Yehova anawafikitsira akazembe a khamu la nkhondo la mfumu ya Asuri, namgwira Manase ndi zokowera, nammanga matangadza, namuka naye ku Babulo.
12
Ndipo popsinjika iye anapembedza Yehova Mulungu wace, nadzicepetsa kwambiri pamaso pa Mulungu wa makolo ace.
13
Anampempha, ndipo anapembedzeka, namvera kupembedza kwace, nambwezera ku Yerusalemu m'ufumu wace. Pamenepo anadziwa Manase kuti Yehova ndiye Mulungu.
14
Citatha ici tsono iye anaumangira mudzi wa Davide linga lakunja, kumadzulo kwa Gihoni, m'cigwa, mpaka polowera pa cipata cansomba; nazinga Ofeli, nalikweza kwambiri; anaikanso akazembe a nkhondo m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda.
15
Ndipo anacotsa milungu yacilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi m'Yerusalemu, nawataya kunja kwa mudzi.
16
Namanga guwa la nsembe la Yehova, napherapo nsembe zamtendere ndi zoyamika, nalamulira Yuda atumikire Yehova Mulungu wa Israyeli.
17
Koma anthu anapherabe nsembe pamisanje; koma anaziphera Yehova Mulungu wao.
18
Macitidwe ena tsono a Manase, ndi pemphero lace kwa Mulungu wace, ndi mau a alauli akunena naye m'dzina la Yehova Mulungu wa Israyeli, taonani, zalembedwa m'niacitidwe a mafumu a Israyeli.
19
Pemphero lace lomwe, ndi m'mene Mulungu anapembedzeka naye, ndi chimo lace lonse, ndi kulakwa kwace, ndi apo anamanga misanje, naimika zifanizo ndi mafano osema asanadzicepetse, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Hozai.
20
Momwemo Manase anagona ndi makolo ace, namuika m'nyumba mwace mwace; ndi Amoni mwana wace anakhala mfumu m'malo mwace.
21
Amoni ndiye wa zaka makumi awiri mphambu ziwiri polowa ufumu wace, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka ziwiri.
22
Ndipo anacita coipa pamaso pa Yehova, monga umo anacitira Manase atate wace; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate wace, nawatumikira.
23
Koma sanadzicepetsa pamaso pa Yehova, monga umo anadzicepetsera Manase atate wace; koma Amoni amene anacurukitsa kuparamula kwace.
24
Ndipo anyamata ace anampangira ciwembu, namupha m'nyumba yace yace.
25
Koma anthu a m'dziko anapha onse adampangira ciwembu mfumu Amoni; ndi anthu a m'dziko analonga Yosiya mwana wace akhale mfumu m'malo mwace.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36