bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ecclesiastes 1
Ecclesiastes 1
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 2 →
1
MAU a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu.
2
Zacabecabe, ati Mlaliki; zacabecabe zonse ndi cabe.
3
Kodi nchito zace zonse munthu asauka nazo zimpindulira ciani?
4
Mbadwo wina opita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse,
5
inde dzuwa lituruka, nililowa, nilifulumira komwe linaturukako.
6
Kulowa kumwela ndi kuzungulira: kumpoto zungulire zungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ace.
7
Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
8
Zinthu zonse zilemetsa; munthu sakhoza kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva.
9
Comwe cinaoneka cidzaonekanso; ndi comwe cinacitidwa cidzacitidwanso; ndipo palibe kanthu katsopano pansi pano.
10
Kodi pali kanthu unganene kuti, Taona katsopano aka? Kanalipo kale, kale lomwe tisanabadwe ife.
11
Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zirinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.
12
Ine Mlaliki ndinali mfumu ya: Israyeli m'Yerusalemu.
13
Ndipo ndinapereka mtima kufunafuna ndi nzeru, ndi kulondetsa zonse zimacitidwa pansi pa thambo; nchito yobvuta imeneyi Mulungu apatsa ana a anthu akasauke nayo.
14
Ndaona nchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
15
Cokhotakhota sicingaongokenso; ndipo coperewera sicingawerengedwe.
16
Ndinalankhula ndi mtima wanga, ndi kuti, Taona, ndakuza ndi kudzienjezera nzeru koposa onse anakhala m'Yerusalemu ndisanabadwe ine; inde mtima wanga wapenyera kwambiri nzeru ndi cidziwitso.
17
Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti icinso cingosautsa mtima.
18
Pakuti m'nzeru yambiri muli cisoni cambiri; ndi yemwe aenjezera cidziwitso aenjezera zowawa.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12