bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ecclesiastes 4
Ecclesiastes 4
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 5 →
1
Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimacitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.
2
Ndipo ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe;
3
inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone nchito yoipa yocitidwa kunja kuno.
4
Ndiponso ndinapenyera mabvuto onse ndi nchito zonse zompindulira bwino, kuti cifukwa ca zimenezi anansi ace acitira munthu nsanje. Icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
5
Citsiru cimanga manja ace, nicidya nyama yace yace.
6
Dzanja limodzi lodzala pali mtendere liposa manja awiri oti tho pali bvuto ndi kungosautsa mtima.
7
Pamenepo ndinabwera ndi kupenyera zacabe kunja kuno.
8
Pali mmodzi palibe waciwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma nchito yace yonse iribe citsiriziro, ngakhale diso lace silikhuta cuma. Samati, Ndigwira nchito ndi kumana moyo wanga zabwino cifukwa ca yani? Icinso ndi cabe, inde, bvuto lalikuru.
9
Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'nchito zao.
10
Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzace; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.
11
Ndiponso awiri akagona limodzi afunditsana; koma mmodzi pa yekha kodi adzafunditsidwa bwanji?
12
Ndipo wina akamlaka mmodziyo, awiri adzacirimika; ndipo cingwe ca nkhosi zitatu siciduka msanga.
13
Mnyamata wosauka ndi wanzeru apambana mfumu yokalamba ndi yopusa, imene sifunanso kulangidwa mwambo.
14
Pakuti aturuka m'nyumba yandende kulowa ufumu; komanso yemwe abadwa m'dziko lace asauka.
15
Ndinapenyera anthu onse amoyo akuyenda kunja kuno, kuti anali ndi mwana, waciwiri, amene adzalowa m'malo mwace.
16
Anthu onse sawerengeka, ngakhale onsewo anawalamulira; koma amene akudza m'mbuyo sadzakondwera naye. Icinso ndi cabe nicisautsa mtima.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12