bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ecclesiastes 3
Ecclesiastes 3
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 4 →
1
Kanthu kali konse kali ndi nthawi yace ndi cofuna ciri conse ca pansi pa thambo ciri ndi mphindi yace;
2
mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzyala ndi mphindi yakuzula zobzyalazo;
3
mphindi yakupha ndi mphindi yakuciza; mphindi yakupasula ndi mphindi yakumanga;
4
mphindi yakugwa misozi ndi mphindi yakuseka; mphindi yakulira ndi mphindi yakubvina;
5
mphindi yakutaya miyala ndi mphindi yakukundika miyala; mphindi yakufungatirana ndi mphindi yakuleka kufungatirana;
6
mphindi yakufunafuna ndi mphindi yakumwazika; mphindi yakusunga ndi mphindi yakutaya;
7
mphindi yakung'amba ndi mphindi yakusoka; mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula;
8
mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere.
9
Wogwira nchito aona phindu lanji m'comsautsaco?
10
Ndaona bvuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti abvutidwe nalo.
11
Cinthu ciri conse anacikongoletsa pa mphindi yace; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse nchito Mulungu wazipanga ciyambire mpaka citsiriziro.
12
Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kucita zabwino pokhala ndi moyo.
13
Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m'nchito zace zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.
14
Ndidziwa kuti zonse Mulungu azicita zidzakhala kufikira nthawi zonse; sungaonjezepo kanthu, ngakhale kucotsapo; Mulungu nazicita kuti anthu akaope pamaso pace.
15
Cocomwe cinaoneka, cirikuonekabe; ndi comwe cidzaoneka cinacitidwa kale; Mulungu anasanthula zocitidwa kale.
16
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zaipa; ndi malo a cilungamo, komweko kuli zoipa.
17
Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi nchito zonse.
18
Ndinati mumtima mwanga, kuti izi zicitika ndi ana a anthu, kuti Mulungu awayese ndi kuti akazindikire eni ace kuti ndiwo nyama za kuthengo.
19
Pakuti comwe cigwera ana a anthu cigweranso nyamazo; ngakhale cowagwera ncimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso; inde onsewo ali ndi mpweya umodzi; ndipo munthu sapambana nyama pakuti zonse ndi cabe,
20
onse apita ku malo amodzi; onse acokera m'pfumbi ndi onse abweranso kupfumbi.
21
Ndani adziwa mzimu wa ana a anthu wakwera kumwamba, ndi mzimu wa nyama wotsikira kunsi ku dziko?
22
M'mwemo ndinazindikira kuti kulibe kanthu kabwino kopambana aka, kuti munthu akondwere ndi nchito zace; pakuti gawo lace ndi limeneli; pakuti ndani adzamfikitsa kuona comwe cidzacitidwa ataca iyeyo?
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12