bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ecclesiastes 6
Ecclesiastes 6
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 7 →
1
Pali coipa ndaciona kunja kuno cifalikira mwa anthu,
2
munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa cuma ndi ulemu, mtima wace susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ici ndi cabe ndi nthenda yoipa,
3
Cinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zace ndi kucuruka, koma mtima wace osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;
4
pakuti ikudza mwacabe, nicoka mumdima, mdima nukwirira dzina lace.
5
Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;
6
akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita ku malo amodzi?
7
Nchito zace zonse munthu angogwirira m'kamwa mwace, koma mtima wace sukhuta.
8
Pakuti wanzeru ali ndi ciani coposa citsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pa maso pa amoyo ali ndi ciani?
9
Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; icinso ndi cabe ndi kungosautsa mtima.
10
Comwe cinalipo cachedwa dzina lace kale, cidziwika kuti ndiye munthu; sakhoza kulimbana ndi womposa mphamvu.
11
Pokhala zinthu zambiri zingocurukitsa zacabe, kodi anthu aona phindu lanji?
12
Pakuti ndani adziwa comwe ciri cabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wace wacabe umene autsiriza ngati mthunzi? pakuti ndani adzauza munthu cimene cidzaoneka m'tsogolo mwace kunja kuno?
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12