bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Exodus 17
Exodus 17
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 18 →
1
Ndipo khamu lonse la ana a Israyeli linacoka m'cipululu ca Sini, m'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona m'Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.
2
Pamenepo anthu anatsutsana ndi Mose, nati, Tipatseni madzi timwe, Koma Mose ananena nao, Mutsutsana nane bwanji? Muyeseranji Yehova?
3
Ndipo pomwepo anthu anamva ludzu lokhumba madzi; ndi anthu anadandaulira Mose, nati, Munatikwezeranji kucokera ku Aigupto, kudzatipha ife ndi ana athu ndi zoweta zathu ndi ludzu?
4
Ndipo Mose anapfuulira kwa Yehova, ndi kuti, Ndiwacitenji anthuwa? andilekera pang'ono kundiponya miyala.
5
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pita pamaso pa anthu, nutenge pamodzi nawe akuru ena a Israyeli; nutenge m'dzanja mwako ndodo ija unapanda nayo nyanja, numuke.
6
Taona, ndidzaima pamaso pako pathanthwe m'Horebe; ndipo upande thanthwe, nadzaturukamo madzi, kuti anthu amwe. Ndipo Mose anacita comweco pamaso pa akuru a Israyeli.
7
Ndipo anacha dzina la malowo Masa, ndi Meriba, cifukwa ca kutsutsana kwa ana a Israyeli; popezanso anayesa Yehova, ndi kuti, Kodi Yehova ali pakati pa ife, kapena iai?
8
Pamenepo anadza Amaleki, nayambana ndi Israyeli m'Refidimu.
9
Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nuturuke kuyambana naye Amaleki; mawa ndidzaima pamwamba pa citunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.
10
Ndipo Yoswa anacita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleki; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa citunda.
11
Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lace Israyeli analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lace Amaleki analakika.
12
Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ace, wina mbali yina, wina mbali yina; ndi manja ace analimbika kufikira litalowa dzuwa.
13
Ndipo Yoswa anatyola Amaleki ndi anthu ace ndi kuukali kwa lupanga.
14
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ici m'buku, cikhale cikumbutso, nucimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse cikumbukilo ca Amaleki pansi pa thambo.
15
Ndipo Mose anamanga guwa la nsembe, nalicha dzina lace Yehova Nisi:
16
nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleki m'mibadwo mibadwo.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40