bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Exodus 26
Exodus 26
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 27 →
1
Ndipo uzipanga kacisi ndi nsaru zophimba khumi, za bafuta wa thonje losansitsa, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira; uombemo akerubi, nchito ya mmisiri.
2
Utali wace wa nsaru yophimba imodzi ndiwo mikono makumi awiri kudza isanu ndi itatu, ndi kupingasa kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsaru zonse zikhale za muyeso umodzi.
3
Nsaru zisanu zilumikizane yina ndi inzace; ndi nsaru zisanu zina zilumikizane yina ndi inzace.
4
Ndipo uziika magango a nsaru yamadzi m'mphepete mwace mwa nsaru imodzi, ku mkawo wa cilumikizano; nucite momwemo m'mphepete mwace mwa nsaru ya kuthungoya cilumikizano dna.
5
Uziika magango makumi asanu pa nsaru yocingira imodzi, nuikenso magango makumi asanu m'mphepete mwace mwa nsaru ya cilumikizano cina; ndipo magango akomanizane lina ndi linzace.
6
Uzipanganso zokowera makumi asanu zagolidi, ndi kumanga nsaruzo pamodzi ndi zokowerazo; kuti kacisi akhale mmodzi.
7
Ndipo uziomba nsaru zophimba za ubweya wa mbuzi zikhale hema pamwamba pa kacisi; uziomba nsaru khumi ndi imodzi.
8
Utali wace wa nsaru imodzi ndiwo mikono makumi atatu, ndi kupingasa kwace kwa nsaru imodzi ndiko mikono inai; nsarukhumi ndi imodzi zikhale za muyeso womwewo.
9
Nuzisoka pamodzi nsaru zisanu pa zokha ndi nsaru zisanu ndi imodzi pa zokha, nupinde nsaru yacisanu ndi cimodziyo pa khomo la hema.
10
Ndipo uziika magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru imodzi, ya kuthungo ya cilumikizano, ndi magango makumi asanu m'mphepete mwa nsaru ya kuthungo ya cilumikizano cina.
11
Ndipo uzipanga zokowera makumi asanu zamkuwa, ndi kukowetsa zokowerazo m'magangomo, ndi kumanga pamodzi hemalo likhale limodzi.
12
Ndipo cotsalaco pa nsaru za hemalo, hafu yace ya nsaru yotsalirayo, icinge pambuyo pace pa kacisi.
13
Ndi mkono wa pa mbali yino, ndi mkono wa pa mbali inzace, wakutsalira m'utali wace wa nsaru za hemalo, icinge pambali zace za kacisi, mbali yino ndi mbali yina, kumphimba.
14
Ndipo uzipangira hema cophimba ca zikopa za nkhosa zamphongo zonika zofiira, ndi cophimba za zikopa za akatumbu pamwamba pace.
15
Ndipo uzipangira kacisi matabwa oimirika, a mtengo wasitimu.
16
Utali wace wa thabwa limodzi ndiwo mikono khumi, ndi kupingasa kwace kwa thabwali mkono ndi hafu.
17
Pa thabwa limodzi pakhale mitsukwa iwiri, yomangika pamodzi; uzitero pa matabwa onse a kacisi.
18
Ndipo uzipanga matabwa a kacisi, matabwa makumi awiri ku mbali ya kumwela, kumwela.
19
Nuzipanga makamwa makumi anai asiliva pansi pa matabwa makumi awiri; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi kwa mitsukwa yace iwiri, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina kwa mitsukwa yace iwiri;
20
ndi pa mbali yace yina ya kacisi, mbali ya kumpoto, pakhale matabwa makumi awiri; ndi makamwa asiliva makumi anai;
21
makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.
22
Ndipo uzipanga matabwa asanu ndi limodzi kwa mbali ya kacisi ya kumbuyo kumadzulo.
23
Nupange matabwa awiri a ngondya za kacisi za kumbuyo.
24
Ndipo akhale ophatikizika pamodzi patsinde, nakhalenso ophatikizika pamodzi kumutu kwace ndi mphete imodzi; azitero onse awiri; azikhala a ngondya ziwiri.
25
Ndipo pakhale matabwa asanu ndi atatu, ndi makamwa ao asiliva, ndiwo makamwa khumi mphambu asanu ndi limodzi; makamwa awiri pansi pa thabwa limodzi, ndi makamwa awiri pansi pa thabwa lina.
26
Ndipo uzipanga mitanda ya mtengo wasitimu; isanu ya matabwa a pa mbali yina ya kacisi,
27
ndi mitanda isanu ya matabwa a Pel mbali yina ya kacisi, ndi mitanda isanu ya matabwa a pa mbali ya kacisi ya kumbuyo kumadzulo.
28
Ndi mtanda wa pakati pa matabwa ufikire kuthungo.
29
Ndipo uzikuta matabwa ndi golidi, ndi kupanga mphete zao zagolidi zopisamo mitandayo; uzikutanso mitandayo ndi golidi.
30
Ndipo uutse kacisi monga mwa makhalidwe ace amene anakusonyeza m'phiri.
31
Ndipo uziomba nsaru yocinga ya thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi la bafuta wa thonje losansitsa, aiombe ndi akerubi nchito ya mmisiri;
32
ndipo uicinge pa mizati inai ya mitengo wasitimu, zokuta ndi golidi; zokowera zao zikhale zagolidi, ndi makamwa anai asiliva.
33
Ndipo uzicinga nsaru yocinga pa zokowerazo, nulowetse likasa la mboni kukati kwa nsaru yocinga; ndipo nsaru yocingayo idzakugawirani pakati pa malo opatulika ndi malo opatulikitsa.
34
Ndipo uziika cotetezerapo pa likasa la mboni, m'malo opatulikitsa.
35
Nuziika gomelo kunja kwa nsaru yocinga, ndi coikapo nyali pandunji pa gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi; koma uike gomelo pa mbali ya kumpoto,
36
Ndipo uziomba nsaru yotsekera pa khomo la bema, ya lakuda, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya wopikula.
37
Ndipo uzipangira nsaru yotsekerayo nsanamira zisanu za mtengo wasitimu, ndi kuzikuta ndi golidi; zokowera zao zikhale zagolidi; nuziyengera makamwa asanu amkuwa.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40