bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Exodus 40
Exodus 40
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2
Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse kacisi wa cihema cokomanako.
3
Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nucinge likasalo ndi nsaru yocingayo.
4
Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zace; ulongenso coikapo nyalico, ndi kuyatsa nyali zace.
5
Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lazolidi cakuno ca likasa la mboni, numange pakacisi nsaru yotsekera pakhomo.
6
Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la kacisi wa cihema cokomanako.
7
Ukaikenso mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi.
8
Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo.
9
Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao kacisi, ndi zonse ziri m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse; ndipo adzakhala wopatulika.
10
Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulikitsa.
11
Udzozenso mkhate ndi tsinde lace, ndi kuupatula.
12
Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi.
13
Nubveke Aroni cobvala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatwa andicitire Ine nchito ya nsembe.
14
Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati;
15
nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andicitire nchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao.
16
Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anacita.
17
Ndipo kunali, mwezi woyamba wa caka caciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa kacisi.
18
Ndipo Mose anautsa kacisi, nakhazika makamwa ace, naimika matabwa ace, namangapo mitanda yace, nautsa mizati ndi nsanamira zace.
19
Ndipo anayalika hema pamwamba pa kacisi, naika cophimba ca cihema pamwamba pace; monga Yehova adamuuza Mose.
20
Ndipo anatenga mboniyo, naiika mlikasa, napisa mphiko palikasa, naika cotetezerapo pamwamba pa likasa;
21
nalowa nalo likasa m'kacisi, napacika nsaru yocinga, nacinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose.
22
Ndipo anaika gomelo m'cihema cokomanako, pa mbali ya kumpoto ya kacisi, kunja kwa nsaru yocinga.
23
Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
24
Ndipo anaika coikapo nyali m'cihema cokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi.
25
Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
26
Ndipo anaika guwa la nsembe lagolidi m'cihema cokomanako cakuno ca nsaru yocinga;
27
nafukizapo cofukiza ca pfungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose.
28
Ndipo anapacika kukacisi nsaru yotsekera pakhomo.
29
Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la kacisi wa cihema cokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose.
30
Ndipo anaika mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba.
31
Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ace amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo;
32
pakulowa iwo m'cihema cokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose.
33
Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa cihema ndi guwa la nsembe, napacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza nchitoyi.
34
Pamenepo mtambo unaphimba cihema cokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisiyo.
35
Ndipo Mose sanathe kulowa m'cihema cokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisi.
36
Ndipo pakukwera mtambo kucokera kukacisi, ana a Israyeli amayenda maulendo ao onse;
37
koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera.
38
Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pakacisi msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israyeli, m'maulendo ao onse.
← Chapter 39
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40