bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Exodus 24
Exodus 24
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 25 →
1
Ndipo iye ananena ndi Mose, Ukwere kudza kwa Yehova, iwe ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri; ndipo mugwadire pakudza kutali;
2
ndipo Mose yekha ayandikire kwa Yehova; koma asayandikire iwowa; ndi anthunso asakwere naye.
3
Ndipo Mose anadza nafotokozera anthu mau onse a Yehova, ndi masveruzo onse; ndipo anthu onse anabvomera pamodzi, nati, Mau onse walankhula Yehova tidzacita.
4
Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde pa phiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.
5
Ndipo anatuma ana a Israyeli a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, zang'ombe.
6
Ndipo Mose anagawa mwaziwo, nathira wina m'zotengera, nawaza wina pa guwa la nsembe.
7
Ndipo anatenga buku la Cipangano, nawerenga m'makutu a anthu; ndipo iwo anati, Zonse zimene Yehova walankhula tidzacita, ndi kumvera.
8
Ndipo Mose anatenga mwaziwo, nawaza pa anthu, nati, Taonani mwazi wa cipangano, cimene Yehova anacita nanu, kunena za mau awa onse,
9
Ndipo Mose ndi Aroni, Nadabu ndi Abihu, ndi akuru a Israyeli makumi asanu ndi awiri anakwerako;
10
ndipo anapenya Mulungu wa Israyeli; ndipo pansi pa mapazi ace panali ngati mayalidwe oyera a miyala yasafiri, ndi ngati thupi la thambo loti mbe.
11
Koma sanaturutsa dzanja lace pa akuru a ena a Israyeli; ndipo anapenya Mulungu, nadya, namwa.
12
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ukwere kudza kwa Ine m'phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi cilamulo ndi malamulo, ndawalembera kuti uwalangize.
13
Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wace; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.
14
Ndipo anati kwa akuru, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.
15
Ndipo Mose anakwera m'phirimo, ndi mtambo unaphimba phirilo,
16
Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe pa phiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lacisanu ndi ciwiri iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.
17
Ndipo maonekedwe a ulemerero wa Yehova anali ngati mota wonyeketsa pamwamba pa phiri, pamaso pa ana a Israyeli.
18
Ndipo Mose analowa m'kati mwa mtambo, nakwera m'phirimo; ndipo Mose anakhala m'phiri masiku makumi anai usana ndi usiku.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40