bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Song of Solomon 2
Song of Solomon 2
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 3 →
1
Ndine duwa lofiira la ku Saroni, Ngakhale kakombo wa kuzigwa.
2
Ngati kakombo pakati pa minga Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana akazi.
3
Ngati maula pakati pa mitengo ya m'nkhalango, Momwemo wokondedwa wanga pakati pa ana amuna. Ndinakondwa pakukhala pa mthunzi wace, Zipatso zace zinatsekemera m'kamwa mwanga.
4
Anandifikitsa ku nyumba ya vinyo, Mbendera yace yondizolimira inali cikondi.
5
Mundilimbikitse ndi mphesa zouma, munditonthoze mtima ndi maula, Pakuti ndadwala ndi cikondi.
6
Dzanja lace lamanzere anditsamiritse kumutu, Dzanja lace lamanja ndi kundifungatira.
7
Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, Pali mphoyo, ndi nswala za kuthengo, Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi, Mpaka cikafuna mwini.
8
Mau a wokondedwa wanga mnyamatayo! Taona, adza, Alikulumpha pamapiri, alikujidimuka pazitunda.
9
Wokondedwa wanga akunga mphoyo, pena mwana wa mbawala: Taona, aima patseri pa khoma pathu, Apenyera pazenera, Nasuzumira pamade.
10
Wokondedwa wanga analankhula, nati kwa ine, Tauka, bwenzi langa, wokongola wanga, tiye.
11
Pakuti, taona, cisanu catha, Mvula yapita yaleka;
12
Maluwa aoneka pansi; Nthawi yoyimba mbalame yafika, Mau a njiwa namveka m'dziko lathu;
13
Mkuyu uchetsa nkhuyu zace zosakhwima, Mipesa niphuka, Inunkhira bwino. Tauka, bwenzi langa, wokongola wangawe, tiyetu.
14
Nkhunda yangawe, yokhala m'ming'alu ya thanthwe, mobisika motsetsereka, Ndipenye nkhope yako, ndimve manako; Pakuti mau ako ngokoma, nkhope yako ndi kukongola.
15
Mutigwirire ankhandwe, ngakhale ang'ono, amene akuononga minda yamipesa; Pakuti m'minda yathu yamipesa muphuka biriwiri.
16
Wokondedwa wanga ndi wa ine, ine ndine wace: Aweta zace pakati pa akakombo,
17
Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha, Bwera, bwenzi langawe, nukhale ngati mphoyo pena mwana wa mbawala Pa mapiri a mipata.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8