bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Song of Solomon 7
Song of Solomon 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 8 →
1
Ha, mapazi ako akongola m'zikwakwata, Mwana wamkaziwe wa mfumu! Pozinga m'cuuno mwako pakunga zonyezimira, Nchito ya manja a mmisiri waluso.
2
Pamcombo pako pakunga cikho coulungika, Cosasowamo vinyo wosanganika: Pamimba pako pakunga mulu wa tirigu Wozingidwa ndi akakombo.
3
Maere ako akunga ana awiri a nswala Anabadwa limodzi.
4
Khosi lako likunga nsanja yaminyanga; Maso ako akunga matawale a ku Hesiboni, A pa cipata ca Batirabimu; Mphuno yako ikunga nsanja ya ku Lebano Imene iloza ku Damasiko.
5
Mutu wako ukunga Karimeli, Ndi tsitsi la pamtu pako likunga nsaru yakuda; Mfumu yamangidwa ndi nkhata zace ngati wamsinga.
6
Ha, ndiwe wokongola ndi wofunika, Bwenziwe, m'zokondweretsa!
7
Msinkhu wakowu ukunga mlaza, Maere ako akunga matsango amphesa,
8
Ndinati, Ndikakwera pamlazapo, Ndikagwira nthambi zace: Maere ako ange ngati matsango amphesa, Ndi kununkhira kwa mpweya wako ngati maula;
9
M'kamwa mwako munge ngati vinyo woposa, Womeza tseketeke bwenzi langa, Wolankhulitsa milomo ya ogona tulo.
10
Ndine wa wokondedwa wanga mnyamatayo, Ndine amene andifunayo.
11
Tiye, bwenzi langa, tinke kuminda; Titsotse m'miraga.
12
Tilawire kunka ku minda yamipesa; Tiyang'ane ngati mpesa waphuka, kunje ndi kuonetsa zipatso, Makangaza ndi kutuwa maluwa ace; Pompo ndidzakupatsa cikondi canga,
13
Mandimu anunkhira, Ndi pamakomo pathu zipatso zabwino, za mitundu mitundu, zakale ndi zatsopano, Zimene ndakukundikira iwe, wokondedwa wanga.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8