bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Song of Solomon 8
Song of Solomon 8
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
1
Mwenzi utakhala ngati mlongwanga, Woyamwa pa bere la amai! Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona; Osandinyoza munthu.
2
Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai, Kuti andilange mwambo; Ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa, Ndi madzi a makangaza anga.
3
Dzanja lamanzere lace akadanditsamiritsa kumutu, Lamanja lace ndi kundifungatira.
4
Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, Muutsiranji, mugalamutsiranji cikondi, Cisanafune mwini.
5
Ndaniyu acokera kucipululu, Alikutsamira bwenzi lace? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amako anali mkusauka nawe, Pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.
6
Undilembe pamtima pako, mokhoma cizindikilo, nundikhomenso cizindikilo pamkono pako; Pakuti cikondi cilimba ngati imfa; Njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwace ndi kung'anima kwa moto, Ngati mphezi ya Yehova,
7
Madzi ambiri sangazimitse cikondi, Ngakhale mitsinje yodzala kucikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yace ngati sintho la cikondi, Akanyozedwa ndithu.
8
Tiri ndi mlongwathu wamng'ono, Alibe maere; Ticitirenji mlongwathu Tsiku lokhoma unkhoswe wace?
9
Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva: Ngati ndiye citseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.
10
Ndine khoma, maere anga akunga nsanja zace: Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.
11
Solomo anali ndi munda wamipesa ku Baalahamoni; Nabwereka alimi mundawo; Yense ambwezere ndalama cikwi cifukwa ca zipatso zace.
12
Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu; Naco cikwico, Solomo iwe, Koma olima zipatso zace azilandira mazana awiri.
13
Namwaliwe wokhala m'minda, Anzake amvera mau ako: Nanenso undimvetse.
14
Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga, Dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala Pa mapiri a mphoka,
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8