bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Song of Solomon 3
Song of Solomon 3
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 4 →
1
Usiku pamphasa panga ndinamfunafuna amene moyo wanga umkonda: Ndinamfunafuna, koma osampeza.
2
Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mudzi, M'makwalala ndi m'mabwalo ace, Ndimfunefune amene moyo wanga umkonda: Ndimfunafuna, koma osampeza.
3
Alonda akuyendayenda m'mudzi anandipeza: Ndinati, Kodi munamuona amene moyo wanga umkonda?
4
Nditawapitirira pang'ono, Ndinampeza amene moyo wanca umkonda: Ndinamgwiriziza, osamfumbatula, Mpaka nditamlowetsa m'nyumba ya amai, Ngakhale m'cipinda ca wondibala.
5
Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, Pali mphoyo, ndi nswala ya kuthengo, Kuti musautse, ngakhale kugalamutsa cikondi, Mpaka cikafuna mwini.
6
Ndaniyu akwera kuturuka m'cipululu ngati utsi wa tolo, Wonunkhira ndi nipa ndi mtanthanyerere, Ndi zonunkhiritsa zonse za wogulitsa?
7
Taonani, ndi macila a Solomo; Pazingapo amuna amphamvu makumi asanu ndi limodzi, A mwa ngwazi za Israyeli.
8
Onsewo agwira lupanga, nazolowera nkhondo: Yense ali ndi lupanga lace pancafu pace, Cifukwa ca upandu wa usiku.
9
Solomo mfumu anadzipangira macila okhalamo tsonga Ndi matabwa a ku Lebano.
10
Anapanga timilongoti tace ndi siliva, Ca pansi pace ndi golidi, mpando wace ndi nsaru yakuda, Pakati pace panayalidwa za cikondi ca ana akazi a ku Yerusalemu.
11
Turukani, ana akazi inu a Ziyoni, mupenye Solomo mfumu, Ndi korona amace anambveka naye tsiku la ukwati wace, Ngakhale tsiku lakukondwera mtima wace.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8