bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Kings 14
2 Kings 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 15 →
1
Chaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.
2
Ndiye wa zaka makumi awiri ndi zisanu polowa ufumu; nakhala mfumu zaka makumi awiri mphambu zisanu ndi zinai m'Yerusalemu; dzina la make ndiye Yehowadani wa ku Yerusalemu.
3
Ndipo anachita zoongoka pamaso pa Yehova, koma wosanga Davide kholo lake; nachita monga mwa zonse anazichita Yowasi atate wake.
4
Koma misanje sanaichotse; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.
5
Ndipo kunali, utakhazikika ufumu m'dzanja lake, anakantha anyamata ake amene adakantha mfumu atate wake;
6
koma ana a ambandawo sanawaphe, monga mwalembedwa m'buku la chilamulo cha Mose, m'mene adalamulira Yehova, ndi kuti, Atate asaphedwere ana, kapena ana kuphedwera atate; koma yense afere kulakwa kwa iye yekha.
7
Anapha Aedomu m'Chigwa cha Mchere zikwi khumi, nalanda Sela ndi nkhondo, nautcha dzina lake Yokotele mpaka lero lino.
8
Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso.
9
Natumiza Yehowasi mfumu ya Israele kwa Amaziya mfumu ya Yuda, ndi kuti, Mtungwi wa ku Lebanoni unatumiza mau kwa mkungudza wa ku Lebanoni, ndi kuti, Mpatse mwana wanga wamwamuna mwana wako wamkazi akhale mkazi wake; ndipo inapitapo nyama ya kuthengo ya ku Lebanoni, nipondereza mtungwiwo.
10
Wakanthadi Aedomu, koma mtima wako wakukweza; ulemekezeke, nukhale kwanu; udziutsiranji tsoka, ungagwe iwe ndi Yuda pamodzi nawe;
11
Koma Amaziya sanamvere. Motero anakwera Yehowasi mfumu ya Israele, ndipo iye ndi Amaziya mfumu ya Yuda anapenyana maso ku Betesemesi, ndiwo wa Yuda.
12
Nakanthidwa Yuda pamaso pa Israele, nathawira yense kuhema kwake.
13
Ndipo Yehowasi mfumu ya Israele anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi mwana wa Ahaziya, ku Betesemesi, nadza ku Yerusalemu, nagamula linga la Yerusalemu kuyambira chipata cha Efuremu kufikira chipata cha kungodya, mikono mazana anai.
14
Natenga golide ndi siliva yense, ndi zotengera zonse anazipeza m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha m'nyumba ya mfumu, achikole omwe; nabwera kunka ku Samariya.
15
Machitidwe ena tsono a Yehowasi adazichita, ndi mphamvu yake, ndi umo analimbana naye Amaziya mfumu ya Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
16
Nagona Yehowasi ndi makolo ake, namuika m'Samariya pamodzi ndi mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Yerobowamu mwana wake.
17
Ndipo Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo, atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israele, zaka khumi ndi zisanu.
18
Machitidwe ena tsono a Amaziya, sanalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
19
Ndipo anamchitira chiwembu m'Yerusalemu, nathawira iye ku Lakisi; koma anatumiza akumtsata ku Lakisi, namupha komweko.
20
Nabwera naye pa akavalo, namuika ku Yerusalemu pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide.
21
Ndipo anthu onse a Yuda anatenga Azariya, (ndiye Uziya), ndiye wa zaka khumi mphambu zisanu ndi chimodzi, namlonga ufumu m'malo mwa atate wake Amaziya.
22
Anamanga Elati, naubweza kwa Yuda, mfumuyo itagona ndi makolo ake.
23
Chaka chakhumi ndi zisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele analowa ufumu wake m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi anai mphambu chimodzi.
24
Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa zonse za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
25
Anabweza malire a Israele kuyambira polowera ku Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, monga mwa mau a Yehova Mulungu wa Israele, amene ananena ndi dzanja la mtumiki wake Yona mwana wa Amitai mneneriyo, ndiye wa Gatihefere.
26
Pakuti Yehova anapenya kuti kuzunzika kwao kwa Israele nkowawa ndithu; popeza panalibe womangika kapena womasuka, ndipo panalibe womthandiza Israele.
27
Ndipo Yehova sadanena kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yowasi.
28
Machitidwe ena tsono a Yerobowamu, ndi zonse anazichita, ndi mphamvu yake, umo anachita nkhondo, nabweza kwa Israele Damasiko ndi Hamati amene anali a Yuda, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
29
Ndipo Yerobowamu anagona ndi makolo ake, ndiwo mafumu a Israele; nakhala mfumu m'malo mwake Zekariya mwana wake.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25