bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Kings 9
2 Kings 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 10 →
1
Ndipo Elisa mneneriyo anaitana mmodzi wa ana a aneneri, nanena naye, Udzimangire m'chuuno, nutenge nsupa iyi ya mafuta m'dzanja mwako, numuke ku Ramoti Giliyadi.
2
Ndipo ukafikako, ukaunguzeko Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi, nulowe numnyamukitse pakati pa abale ake, nupite naye ku chipinda cham'katimo.
3
Nutenge nsupa ya mafutayo, nuwatsanulire pamutu pake, nunene, Atero Yehova, Ndakudzoza iwe ukhale mfumu pa Israele. Utatero, tsegula pakhomo, nuthawe osachedwa,
4
Pamenepo mnyamatayo, ndiye mneneri, anamuka ku Ramoti Giliyadi.
5
Nalowa, ndipo taonani, akazembe a khamu alikukhala pansi; nati iye, Ndili ndi mau kwa inu, kazembe. Nati Yehu, Kwa yani wa ife tonse? Nati iye, Kwa inu, kazembe.
6
Nanyamuka, nalowa m'nyumba; ndipo anatsanulira mafutawo pamutu pake, nanena naye, Atero Yehova Mulungu wa Israele, Ndakudzoza ukhale mfumu ya pa anthu a Yehova, ndiwo Aisraele.
7
Nudzakantha nyumba ya Ahabu mbuye wako, kuti ndibwezere chilango cha mwazi wa atumiki anga aneneri, ndi mwazi wa atumiki onse a Yehova, dzanja la Yezebele.
8
Popeza nyumba yonse ya Ahabu idzaonongeka, ndipo ndidzalikhira Ahabu ana amuna onse womangika ndi womasuka m'Israele.
9
Ndipo ndidzalinganiza nyumba ya Ahabu ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya.
10
Ndipo agalu adzamudya Yezebele pa dera la Yezireele, wopanda wina wakumuika. Pamenepo anatsegula pakhomo, nathawa.
11
Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake.
12
Nati iwo, Kunama uku; utifotokozere tsono. Nati iye, Anati kwa ine chakutichakuti; ndi kuti, Atero Yehova, Ndakudzoza mfumu pa Israele.
13
Nafulumira iwo, nagwira yense chofunda chake, nachiyala pokhala iye pachiunda, naomba lipenga, nati, Yehu ndiye mfumu.
14
Motero Yehu mwana wa Yehosafati mwana wa Nimisi anapandukira Yoramu. Tsono Yoramu atalindira ku Ramoti Giliyadi, iye ndi Aisraele onse, chifukwa cha Hazaele mfumu ya Aramu;
15
koma mfumu Yoramu adabwera ku Yezireele ampoletse mabala ake anamkantha Aaramu, muja adalimbana naye Hazaele mfumu ya Aramu. Nati Yehu, Ukatero mtima wanu, asapulumuke mmodzi yense kutuluka m'mudzi kukafotokozera m'Yezireele.
16
Nayenda Yehu m'galeta, namuka ku Yezireele, popeza Yoramu anagonako; ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatsikira kukamuona Yoramu.
17
Ndipo mlonda ali chilili pachilindiro m'Yezireele, naona gulu la Yehu lilinkudza, nati, Ndiona gulu. Nati Yoramu, Tenga wapakavalo, numtumize akomane nao, nanene, Mtendere kodi?
18
Ndipo anamuka wapakavalo kukomana naye, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga. Ndi mlonda anawafotokozera kuti, Mthenga wawafika, koma wosabwera.
19
Pamenepo anatumiza wina wapakavalo, nawafika, nati, Atero mfumu, Mtendere kodi? Nati Yehu, Ngwanji mtendere, tembenukira m'mbuyo mwanga.
20
Ndi mlonda anafotokozera, kuti, Wawafika, koma wosabwera; ndipo kuyendetsako kukunga kuyendetsa kwa Yehu mwana wa Nimisi, pakuti ayendetsa moyaluka.
21
Nati Yoramu, Manga. Namanga galeta wake. Ndipo Yoramu mfumu ya Israele ndi Ahaziya mfumu ya Yuda anatuluka yense m'galeta wake, natuluka kukakomana ndi Yehu, nakomana naye pa munda wa Naboti m'Yezireele.
22
Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele?
23
Natembenuza Yoramu manja ake, nathawa, nati kwa Ahaziya, Chiwembu, Ahaziya.
24
Nafa nao Yehu uta wake, nalasa Yoramu pachikota, nutuluka muvi pa mtima wake, naonyezeka iye m'galeta wake.
25
Nati Yehu kwa Bidikara kazembe wake, Mnyamule, numponye m'munda wa Naboti wa ku Yezireele; pakuti kumbukira m'mene ine ndi iwe tinali pa akavalo athu pamodzi kutsata Ahabu atate wake, Yehova anamsenzetsa katundu uyu.
26
Ndapenyadi dzulo mwazi wa Naboti ndi mwazi wa ana ake, ati Yehova; ndipo ndikubwezera pamunda pano, ati Yehova. Mtengeni tsono, mumponye pamundapo, monga mwa mau a Yehova.
27
Koma pochiona ichi Ahaziya mfumu ya Yuda anathawa njira ya ku Betigahani. Namtsata Yehu, nati, Mumkanthe uyonso pagaleta; namkantha pa chikweza cha Guri chili pafupi pa Ibleamu. Nathawira iye ku Megido, namwalira komweko.
28
Ndipo anyamata ake anamnyamulira pagaleta kunka naye ku Yerusalemu, namuika ku manda ake pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide.
29
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chimodzi cha Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya analowa ufumu pa Yuda.
30
Ndipo pofika Yehu ku Yezireele, Yezebele anamva, nadzikometsera m'maso, naluka tsitsi lake, nasuzumira pazenera.
31
Ndipo polowa Yehu pachipata, mkaziyo anati, Mtendere kodi Zimiri, iwe wakupha mbuyako?
32
Koma anakweza maso ake kuzenera, nati, Ali ndi ine ndani? Ndani? Nampenyererako adindo awiri kapena atatu.
33
Nati iye, Mgwetsereni pansi. Namgwetsera pansi, nuwazikako mwazi wake pakhoma ndi pa akavalo, nampondereza iye pansi.
34
Ndipo atalowa, anadya namwa, nati, Kampenyeni tsono mkazi wotembereredwa uyu, nimumuike; popeza ndiye mwana wa mfumu.
35
Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.
36
Nabwerera iwo, namfotokozera. Nati iye, Ndiwo mau a Yehova ananenawo mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, ndi kuti, Pa munda wa Yezireele agalu adzadya mnofu wa Yezebele;
37
ndi thupi la Yezebele lidzakhala ngati ndowe pamunda m'dera la Yezireele, kuti sadzati, Ndi Yezebele uyu.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25