bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Kings 20
2 Kings 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 21 →
1
Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.
2
Pamenepo anatembenuzira nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, ndi kuti,
3
Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.
4
Ndipo kunali, asanatulukire Yesaya m'kati mwa mudzi, anamdzera mau a Yehova, ndi kuti,
5
Bwerera, nunene kwa Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga, Atero Yehova Mulungu wa Davide kholo lako, Ndamva pemphero lako, ndapenya misozi yako; taona, ndidzakuchiritsa, tsiku lachitatu udzakwera kunka kunyumba ya Yehova.
6
Ndipo ndakuonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu; ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'dzanja la mfumu ya Asiriya; ndidzatchinjiriza mudzi uno, chifukwa cha Ine ndekha, ndi chifukwa cha Davide mtumiki wanga.
7
Nati Yesaya, Tenga nchinchi yankhuyu. Naitenga, naiika pafundo, nachira iye.
8
Nati Hezekiya kwa Yesaya, Chizindikiro chake nchiyani kuti Yehova adzandichiza, ndi kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova tsiku lachitatu?
9
Nati Yesaya, Chizindikiro ndichi akupatsa Yehova, kuti Yehova adzachichita chonena Iye; kodi mthunzi umuke m'tsogolo makwerero khumi, kapena ubwerere m'mbuyo makwerero khumi?
10
Nati Hezekiya, Kutsikira mthunzi makwerero khumi nkopepuka, kutero ai; koma mthunzi ubwerere makwerero khumi.
11
Nafuulira kwa Yehova Yesaya mneneriyo, nabweza Iye mthunzi m'mbuyo makwerero khumi, ndiwo amene udatsikira pa makwerero a Ahazi.
12
Nthawi ija Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babiloni anatumiza akalata ndi mtulo kwa Hezekiya, popeza adamva kuti adadwala Hezekiya.
13
Ndipo Hezekiya anawamvera, nawaonetsa nyumba yonse ya chuma chake, siliva, ndi golide, ndi zonunkhira, ndi mafuta okometsetsa, ndi nyumba ya zida zake, ndi zonse zopezeka pachuma pake; panalibe kanthu m'nyumba mwake, kapena m'ufumu wake wonse osawaonetsa Hezekiya.
14
Koma Yesaya mneneri anadza kwa mfumu Hezekiya, nati kwa iye, Anatani anthu awa? Anadza kwa inu kufumira kuti? Nati Hezekiya, Afumira dziko la kutali ku Babiloni.
15
Nati iye, Anaona chiyani m'nyumba mwanu? Nati Hezekiya, Zonse za m'nyumba mwanga anaziona, palibe kanthu pachuma changa kosawaonetsa.
16
Ndipo Yesaya anati kwa Hezekiya, Tamverani mau a Yehova.
17
Taonani, akudza masiku kuti zonse za m'nyumba mwako, ndi zokundika makolo ako mpaka lero, zidzatengedwa kunka ku Babiloni, kosasiyidwa kanthu konse, ati Yehova.
18
Nadzatenga ena a ana ako otuluka mwa iwe, amene udzawabala, nadzakhala iwo adindo m'chinyumba cha mfumu ya Babiloni.
19
Pamenepo Hezekiya anati kwa Yesaya, Mau a Yehova udawanena ndi abwino. Natinso, Si momwemo nanga, mtendere ndi choonadi zikakhala masiku anga?
20
Machitidwe ena tsono a Hezekiya, ndi mphamvu yake yonse, ndi umo anamangira dziwe ndi mchera, nautengera mudzi madzi, sizilembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
21
Nagona Hezekiya ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Manase mwana wake.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25