bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
2 Kings 15
2 Kings 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 16 →
1
Chaka cha makumi awiri mphambu zisanu ndi ziwiri cha Yerobowamu mfumu ya Israele, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.
2
Anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka makumi asanu mphambu ziwiri m'Yerusalemu; ndi dzina la make ndiye Yekoliya wa ku Yerusalemu.
3
Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova, monga mwa zonse adazichita atate wake Amaziya.
4
Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje.
5
Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
6
Machitidwe ena tsono a Azariya, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
7
Nagona Azariya ndi makolo ake, namuika ndi makolo ake m'mudzi wa Davide; nakhala mfumu m'malo mwake Yotamu mwana wake.
8
Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yerobowamu anakhala mfumu ya Israele m'Samariya miyezi isanu ndi umodzi.
9
Nachita iye choipa pamaso pa Yehova, monga adachita makolo ake; sanaleke zolakwa zake za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
10
Ndipo Salumu mwana wa Yabesi anamchitira chiwembu, namkantha pamaso pa anthu, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.
11
Machitidwe ena tsono a Zekariya, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
12
Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.
13
Salumu mwana wa Yabesi analowa ufumu wake chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Uziya mfumu ya Yuda, nakhala mfumu mwezi umodzi m'Samariya.
14
Koma anakwera Menahemu mwana wa Gadi kuchokera ku Tiriza, nafika ku Samariya, nakantha Salumu mwana wa Yabesi m'Samariya, namupha; nakhala mfumu m'malo mwake.
15
Machitidwe ena tsono a Salumu ndi chiwembu chake anachichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
16
Pamenepo Menahemu anakantha Tapuwa, ndi onse anali m'mwemo, ndi malire ake kuyambira ku Tiriza; popeza sanamtsegulire pachipata; anaukantha, natumbula akazi onse a pakati okhala m'mwemo.
17
Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi zinai cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi analowa ufumu wake wa Israele, nakhala mfumu zaka khumi m'Samariya.
18
Nachita choipa pamaso pa Yehova masiku ake onse, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
19
Pamenepo Pulo mfumu ya Asiriya anadza kudzamenyana ndi dziko, koma Menahemu anampatsa Pulo matalente a siliva chikwi chimodzi; kuti dzanja lake likhale naye kukhazikitsa ufumu m'dzanja lake.
20
Ndipo Menahemu anasonkhetsa Israele ndalamazi, nasonkhetsa achuma, yense masekeli makumi asanu a siliva, kuti azipereke kwa mfumu ya Asiriya. Nabwerera mfumu ya Asiriya osakhala m'dzikomo.
21
Machitidwe ena tsono a Menahemu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Israele?
22
Nagona Menahemu ndi makolo ake; nakhala mfumu m'malo mwake Pekahiya mwana wake.
23
Chaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka ziwiri.
24
Nachita choipa pamaso pa Yehova, sanaleke zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
25
Ndipo Peka mwana wa Remaliya, kazembe wake, anamchitira chiwembu, nawakantha limodzi mfumu ndi Arigobu ndi Ariye m'Samariya, m'nsanja ya kunyumba ya mfumu; pamodzi ndi iye panali amuna makumi asanu a Giliyadi; ndipo anamupha, nakhala mfumu m'malo mwake.
26
Machitidwe ena tsono a Pekahiya ndi zonse anazichita, taonani zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
27
Chaka cha makumi asanu mphambu ziwiri cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya analowa ufumu wake wa Israele m'Samariya, nakhala mfumu zaka makumi awiri.
28
Nachita choipa pamaso pa Yehova, osaleka zolakwa za Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene analakwitsa nazo Israele.
29
Masiku a Peka mfumu ya Israele anadza Tigilati-Pilesere mfumu ya Asiriya, nalanda Iyoni, ndi Abele-Beti-Maaka, ndi Yanowa, ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Giliyadi, ndi Galileya, dziko lonse la Nafutali; nawatenga andende kunka nao ku Asiriya.
30
Ndipo Hoseya mwana wa Ela anamchitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya, namkantha, namupha, nakhala mfumu m'malo mwake chaka cha makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.
31
Machitidwe ena tsono a Peka, ndi zonse anazichita, taonani, zalembedwa m'buku la machitidwe a mafumu a Israele.
32
Chaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israele, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda analowa ufumu wake.
33
Ndiye wa zaka makumi awiri mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu zaka khumi ndi zisanu ndi chimodzi m'Yerusalemu; ndipo dzina la make ndiye Yerusa mwana wa Zadoki.
34
Nachita iye zoongoka pamaso pa Yehova; anachita monga mwa zonse anazichita atate wake Uziya.
35
Komatu sanaichotse misanje; anthu anapherabe nsembe, nafukiza pamisanje. Iye anamanga chipata cha kumtunda cha nyumba ya Yehova.
36
Machitidwe ena tsono a Yotamu, ndi zonse anazichita, sizinalembedwa kodi m'buku la machitidwe a mafumu a Yuda?
37
Masiku awa Yehova anayamba kutumizira Yuda Rezini mfumu ya Aramu, ndi Peka mwana wa Remaliya, amenyane naye.
38
Ndipo anagona Yotamu ndi makolo ake, namuika pamodzi ndi makolo ake m'mudzi wa Davide kholo lake; nakhala mfumu m'malo mwake Ahazi mwana wake.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25