bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Joshua 12
Joshua 12
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 13 →
1
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene ana a Israele anawakantha, nalanda dziko lao tsidya la Yordani kum'mawa, kuyambira chigwa cha Arinoni, mpaka phiri la Heremoni, ndi chidikha chonse cha kum'mawa;
2
Sihoni mfumu ya Aamori wokhala m'Hesiboni, wochita ufumu kuyambira ku Aroere ndiwo m'mphepete mwa chigwa cha Arinoni, ndi pakati pa chigwa ndi pa Giliyadi wogawika pakati, kufikira mtsinje wa Yaboki, ndiwo malire a ana a Amoni;
3
ndi pachidikha mpaka nyanja ya Kineroti kum'mawa, ndi mpaka nyanja ya kuchidikha, ndiyo Nyanja ya Mchere kum'mawa, njira ya Beteyesimoti; ndi kumwera pansi pa matsikiro a Pisiga.
4
Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basani wotsala wa Arefaimu, wokhala ku Asitaroti ndi ku Ederei,
5
nachita ufumu m'phiri la Heremoni, ndi m'Saleka, ndi m'Basani lonse, mpaka malire a Agesuri, ndi a Maakati, ndi Giliyadi wogawika pakati, malire a Sihoni mfumu ya ku Hesiboni.
6
Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israele anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi fuko la Manase logawika pakati, likhale cholowa chao.
7
Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israele anawakantha tsidya lija la Yordani kumadzulo, kuyambira Baala-Gadi m'chigwa cha Lebanoni mpaka phiri la Halaki lokwera kunka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mafuko a Israele, likhale laolao, monga mwa magawo ao;
8
kumapiri ndi kuchigwa, ndi kuchidikha, ndi kumatsikiro, ndi kuchipululu, ndi kumwera: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:
9
mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Betele, imodzi;
10
mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi;
11
mfumu ya ku Yaramuti, imodzi; mfumu ya ku Lakisi, imodzi;
12
mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi;
13
mfumu ya ku Debiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi;
14
mfumu ya ku Horoma, imodzi; mfumu ya ku Aradi, imodzi;
15
mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi;
16
mfumu ya ku Makeda, imodzi; mfumu ya ku Betele, imodzi;
17
mfumu ya ku Tapuwa, imodzi; mfumu ya ku Hefere, imodzi;
18
mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi;
19
mfumu ya ku Madoni, imodzi; mfumu ya ku Hazori, imodzi;
20
mfumu ya ku Simironi-Meroni, imodzi; mfumu ya ku Akisafu, imodzi;
21
mfumu ya ku Taanaki, imodzi; mfumu ya ku Megido, imodzi;
22
mfumu ya ku Kedesi, imodzi; mfumu ya ku Yokoneamu ku Karimele, imodzi;
23
mfumu ya ku Dori, mpaka ponyamuka pa Dori, imodzi; mfumu ya ku Goimu m'Galileya, imodzi;
24
mfumu ya ku Tiriza, imodzi. Mafumu awa onse ndiwo makumi atatu ndi imodzi.
← Chapter 11
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 13 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24