bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Joshua 21
Joshua 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 22 →
1
Pamenepo akulu a nyumba za atate a Alevi anayandikira kwa Eleazara wansembe, ndi kwa Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa akulu a nyumba za atate a mafuko a ana a Israele;
2
nanena nao ku Silo m'dziko la Kanani, ndi kuti Yehova analamulira mwa dzanja la Mose kuti atipatse midzi yokhalamo ife, ndi mabusa a zoweta zathu.
3
Ndipo ana a Israele anapatsa Alevi, kutapa pa cholowa chao, monga mwa lamulo la Yehova, midzi iyi ndi mabusa ao.
4
Ndipo maere anatulukira mabanja a Akohati; ndipo molota maere ana a Aroni wansembe, ndiwo Alevi, analandira motapa pa fuko la Yuda, ndi pa fuko la Simeoni, ndi pa fuko la Benjamini, midzi khumi ndi itatu.
5
Ndipo ana otsala a Kohati analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Efuremu, ndi pa fuko la Dani, ndi pa fuko la Manase logawika pakati, midzi khumi.
6
Ndipo ana a Geresoni analandira molota maere motapa pa mabanja a fuko la Isakara, ndi pa fuko la Asere, ndi pa fuko la Nafutali, ndi pa fuko la Manase logawika pakati m'Basani, midzi khumi ndi itatu.
7
Ana a Merari, monga mwa mabanja ao, analandira motapa pa fuko la Rubeni, ndi pa fuko la Gadi, ndi pa fuko la Zebuloni midzi khumi ndi iwiri.
8
Motero ana a Israele anapatsa Alevi midzi iyi ndi mabusa ao, molota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose.
9
Ndipo anapatsa motapa pa fuko la ana a Yuda, ndi pa fuko la ana a Simeoni, midzi iyi yotchulidwa maina ao;
10
kuti ikhale ya ana a Aroni a mabanja a Akohati, a ana a Levi, pakuti maere oyamba adatulukira iwowa.
11
Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo.
12
Koma minda ya mudzi ndi milaga yake anapatsa Kalebe mwana wa Yefune, ikhale yake.
13
Ndipo kwa ana a Aroni wansembe anapatsa Hebroni ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzake, ndi Libina ndi mabusa ake;
14
ndi Yatiri ndi mabusa ake, ndi Esitemowa ndi mabusa ake;
15
ndi Holoni ndi mabusa ake, ndi Debiri ndi mabusa ake;
16
ndi Aini ndi mabusa ake, ndi Yuta ndi mabusa ake, ndi Betesemesi ndi mabusa ake; midzi isanu ndi inai yotapira mafuko awiri aja.
17
Ndipo motapira fuko la Benjamini, Gibiyoni ndi mabusa ake, Geba ndi mabusa ake,
18
Anatoti ndi mabusa ake, ndi Alimoni ndi mabusa ake; midzi inai.
19
Midzi yonse ya ana a Aroni, ansembe, ndiyo khumi ndi itatu, ndi mabusa ao.
20
Ndipo mabanja a ana a Kohati, Aleviwo, otsala a ana a Kohati, analandira midzi ya maere ao motapira pa fuko la Efuremu.
21
Ndipo anawapatsa Sekemu ndi mabusa ake ku mapiri a Efuremu, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Gezere ndi mabusa ake;
22
ndi Kibizaimu ndi mabusa ake, Betehoroni ndi mabusa ake; midzi inai.
23
Ndipo motapira fuko la Dani, Eliteke ndi mabusa ake, ndi Gibetoni ndi mabusa ake;
24
Ayaloni ndi mabusa ake, Gatirimoni ndi mabusa ake; midzi inai.
25
Ndipo motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Taanaki ndi mabusa ake, ndi Gatirimoni ndi mabusa ake; midzi iwiri.
26
Midzi yonse ya mabanja a ana otsala a Kohati ndiyo khumi ndi mabusa ao.
27
Ndipo anapatsa ana a Geresoni, a mabanja a Alevi, motapira pa fuko la Manase logawika pakati, Golani m'Basani ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo; ndi Beesetera ndi mabusa ake; midzi iwiri.
28
Ndipo motapira pa fuko la Isakara, Kisiyoni ndi mabusa ake, Daberati ndi mabusa ake;
29
Yaramuti ndi mabusa ake, Enganimu ndi mabusa ake; midzi inai.
30
Ndipo motapira pa fuko la Asere, Misala ndi mabusa ake, Abidoni ndi mabusa ake;
31
Helekati ndi mabusa ake, ndi Rehobu ndi mabusa ake; midzi inai.
32
Ndipo motapira pa fuko la Nafutali, Kedesi m'Galileya ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Hamotidori ndi mabusa ake, ndi Karitani ndi mabusa ake, midzi itatu.
33
Midzi yonse ya Ageresoni monga mwa mabanja ao ndiyo midzi khumi ndi itatu ndi mabusa ao.
34
Ndipo anapatsa kwa mabanja a ana a Merari, otsala a Alevi, motapira pa fuko la Zebuloni, Yokoneamu ndi mabusa ake, ndi Karita ndi mabusa ake,
35
Dimina ndi mabusa ake, Nahalala ndi mabusa ake; midzi inai.
36
Ndipo motapira pa fuko la Rubeni, Bezeri ndi mabusa ake, ndi Yahazi ndi mabusa ake,
37
Kedemoti ndi mabusa ake, ndi Mefaati ndi mabusa ake; midzi inai.
38
Ndipo motapira m'fuko la Gadi, Ramoti m'Giliyadi ndi mabusa ake, ndiwo mudzi wopulumukirako wakupha mnzakeyo, ndi Mahanaimu ndi mabusa ake;
39
Hesiboni ndi mabusa ake, Yazere ndi mabusa ake: yonse pamodzi midzi inai.
40
Yonseyi ndiyo midzi ya ana a Merari monga mwa mabanja ao, ndiwo otsala a mabanja a Alevi; ndipo gawo lao ndilo midzi khumi ndi iwiri.
41
Midzi yonse ya Alevi, pakati pa cholowa cha ana a Israele ndiyo midzi makumi anai kudza isanu ndi itatu, ndi mabusa ao.
42
Midzi iyi yonse inali nao mabusa ao pozungulira pao: inatero midzi iyi yonse.
43
Motero Yehova anawapatsa Israele dziko lonse adalumbiralo kuwapatsa makolo ao: ndipo analilandira laolao, nakhala m'mwemo.
44
Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaima munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.
45
Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24