bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Joshua 15
Joshua 15
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
1
Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.
2
Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera;
3
natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;
4
napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera.
5
Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;
6
nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
7
nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele;
8
nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.
9
Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba pa phiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumidzi ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.
10
Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna;
11
natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.
12
Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.
13
Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
14
Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
15
Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere.
16
Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake.
17
Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.
18
Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pa bulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19
Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20
Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21
Ndipo midzi ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru;
22
ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;
23
ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani;
24
Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;
25
ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori;
26
Amama ndi Sema ndi Molada;
27
ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti;
28
ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya;
29
Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu;
30
ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma;
31
ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana;
32
ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; midzi yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi milaga yao.
33
Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;
34
ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu;
35
Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;
36
ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; midzi khumi ndi inai pamodzi ndi milaga yao.
37
Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi;
38
ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele;
39
Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni;
40
ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi;
41
ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; midzi khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
42
Libina ndi Eteri ndi Asani;
43
ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu;
44
ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao.
45
Ekeroni pamodzi ndi midzi yake ndi milaga yao;
46
kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi milaga yao.
47
Asidodi, midzi yake ndi milaga yake; Gaza, midzi yake ndi milaga yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.
48
Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko;
49
ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri;
50
ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu;
51
ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; midzi khumi ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
52
Arabu, ndi Duma, ndi Esani;
53
ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka;
54
ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; midzi isanu ndi inai pamodzi ndi milaga yao.
55
Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta;
56
ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;
57
Kaini, Gibea ndi Timna; midzi khumi pamodzi ndi milaga yao.
58
Halahulu, Betezuri, ndi Gedori,
59
ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
60
Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; midzi iwiri pamodzi ndi milaga yao.
61
M'chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka;
62
ndi Nibisani, ndi Mudzi wa Mchere, ndi Engedi; midzi isanu ndi umodzi pamodzi ndi milaga yao.
63
Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
← Chapter 14
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 16 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24