bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Romans 11
Romans 11
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 12 →
1
Chifukwa chake ndinena, Mulungu anataya anthu ake kodi? Msatero ai. Pakuti inenso ndili Mwisraele, wa mbeu ya Abrahamu, wa fuko la Benjamini.
2
Mulungu sanataya anthu ake amene Iye anawadziwiratu. Kapena simudziwa kodi chimene lembo linena za Eliya? Kuti anaumirira Mulungu poneneza Israele, kuti,
3
Ambuye, anawapha aneneri anu, nagwetsa maguwa anu a nsembe; ndipo ine ndatsala ndekha, ndipo alikufuna moyo wanga.
4
Koma kuyankha kwa Mulungu kudatani kwa iye? Ndinadzisiyira ndekha anthu amuna zikwi zisanu ndi ziwiri, amene sanagwadira Baala.
5
Choteronso nthawi yatsopano chilipo chotsalira monga mwa kusankha kwa chisomo.
6
Koma ngati kuli ndi chisomo, sikulinso ndi ntchito ai; ndipo pakapanda kutero, chisomo sichikhalanso chisomo.
7
Ndipo chiyani tsono? Ichi chimene Israele afunafuna sanachipeza; koma osankhidwawo anachipeza, ndipo otsalawo anaumitsidwa mtima;
8
monga kunalembedwa kuti, Mulungu anawapatsa mzimu watulo, maso kuti asapenye, ndi makutu kuti asamve, kufikira lero lino.
9
Ndipo Davide akuti, Gome lao likhale kwa iwo, ngati msampha, ndi ngati diwa, ndi monga chokhumudwitsa, ndi chowabwezera chilango;
10
maso ao adetsedwe, kuti asapenye, ndipo muweramitse msana wao masiku onse.
11
Chifukwa chake ndinena, Anakhumudwa kodi kuti agwe? Msatero ai; koma ndi kulakwa kwao chipulumutso chinadza kwa anthu akunja, kudzachititsa iwo nsanje.
12
Ndipo ngati kulakwa kwao, kwatengera dziko lapansi zolemera, ndipo kuchepa kwao kutengera anthu amitundu zolemera; koposa kotani nanga kudzaza kwao?
13
Koma ndilankhula ndi inu anthu amitundu. Popeza ine ndili mtumwi wa anthu amitundu, ndilemekeza utumiki wanga;
14
kuti ngati nkutheka ndikachititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena a iwo.
15
Pakuti ngati kuwataya kwao kuli kuyanjanitsa kwa dziko lapansi, nanga kulandiridwa kwao kudzatani, koma ndithu ngati moyo wakuchokera kwa akufa?
16
Ndipo ngati zoundukula zili zopatulika, choteronso mtanda; ndipo ngati muzu uli wopatulika, choteronso nthambi.
17
Koma ngati nthambi zina zinathyoledwa, ndipo iwe, ndiwe mtengo wa azitona wa kuthengo, unalumikizidwa mwa izo, nugawana nazo za muzu za mafuta ake a mtengowo,
18
usadzitama iwe wekha pa nthambizo: koma ngati udzitama wekha, suli iwe amene unyamula muzu, ai, koma muzu ukunyamula iwetu.
19
Ndipo kapena udzanena, Nthambizo zathyoledwa kuti ine ndikalumikizidwe nao.
20
Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
21
pakuti ngati Mulungu sanaleka nthambi za mtundu wake, inde sadzakuleka iwe.
22
Chifukwa chake onani kukoma mtima ndi kuuma mtima kwake kwa Mulungu: kwa iwo adagwa, kuuma kwake; koma kwa iwe kukoma mtima kwake kwa Mulungu, ngati ukhala chikhalire m'kukoma mtimamo; koma ngati sutero, adzakusadza iwe.
23
Ndipo iwonso, ngati sakhala chikhalire mu kusakhulupirira, adzawalumikizanso, pakuti Mulungu ali wamphamvu yakutha kuwalumikizanso.
24
Pakuti ngati iwe unasadzidwa kumtengo wa azitona wa mtundu wa kuthengo, ndipo unalumikizidwa ndi mtengo wa azitona wabwino, mokaniza makhalidwe ako; koposa kotani nanga iwo, ndiwo nthambi za mtundu wake, adzalumikizidwa ndi mtengo wao womwewo wa azitona?
25
Pakuti sindifuna, abale, kuti mukhale osadziwa chinsinsi ichi, kuti mungadziyese anzeru mwa inu nokha, kuti kuuma mtima kunadza pang'ono pa Israele, kufikira kudzaza kwa anthu amitundu kunalowa;
26
ndipo chotero Israele yense adzapulumuka; monganso kunalembedwa, kuti, Adzatuluka ku Ziyoni Mpulumutsi; Iye adzachotsa zamwano kwa Yakobo:
27
Ndipo ichi ndi chipangano changa ndi iwo, pamene ndidzachotsa machimo ao.
28
Kunena za Uthenga Wabwino, iwo ali ngati adani, chifukwa cha inu; koma kunena za chisankhidwe, ali okondedwa, chifukwa cha makolo.
29
Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.
30
Pakuti monga inunso kale simunamvera Mulungu, koma tsopano mwalandira chifundo mwa kusamvera kwao,
31
choteronso iwo sanamvera tsopano, kuti iwonso akalandire chifundo, chifukwa cha chifundo cha kwa inu.
32
Pakuti Mulungu anatsekera pamodzi onse m'kusamvera, kuti akachitire onse chifundo.
33
Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!
34
Pakuti anadziwitsa ndani mtima wake wa Ambuye? Kapena anakhala mphungu wake ndani?
35
Ndipo anayamba ndani kumpatsa Iye, ndipo adzambwezeranso?
36
Chifukwa zinthu zonse zichokera kwa Iye, zichitika mwa Iye, ndi kufikira kwa Iye. Kwa Iyeyo ukhale ulemerero kunthawi zonse. Amen.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16