bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Romans 9
Romans 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 10 →
1
Ndinena zoona mwa Khristu, sindinama ai, chikumbu mtima changa chichita umboni pamodzi ndine mwa Mzimu Woyera,
2
kuti ndagwidwa ndi chisoni chachikulu ndi kuphwetekwa mtima kosaleka.
3
Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;
4
ndiwo Aisraele; ali nao umwana, ndi ulemerero, ndi mapangano, ndi kupatsa kwa malamulo, ndi kutumikira m'Kachisi wa Mulungu, ndi malonjezo;
5
a iwo ali makolo, ndi kwa iwo anachokera Khristu, monga mwa thupi, ndiye Mulungu wa pamwamba pa zonse wolemekezeka kunthawi zonse. Amen.
6
Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;
7
kapena chifukwa ali mbeu ya Abrahamu, siali onse ana; koma anati, Mwa Isaki, mbeu yako idzaitanidwa.
8
Ndiko kuti, ana a thupi sakhala iwo ana a Mulungu ai; koma ana a lonjezo awerengedwa mbeu yake.
9
Pakuti mau a lonjezo ndi amenewa, Pa nyengo iyi ndidzadza, ndipo Sara adzakhala ndi mwana.
10
Ndipo si chotero chokha, koma Rebekanso, pamene anali ndi pakati pa mmodzi, ndiye kholo lathu Isaki;
11
pakuti anawo asanabadwe, kapena asanachite kanthu kabwino kapena koipa, kuti kutsimikiza mtima kwa Mulungu monga mwa kusankha kukhale, si chifukwa cha ntchito ai, koma chifukwa cha wakuitanayo,
12
chotero kunanenedwa kwa uyo, Wamkulu adzakhala kapolo wa wamng'ono.
13
Inde monga kunalembedwa, Ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau.
14
Ndipo tsono tidzatani? Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ai.
15
Pakuti anati ndi Mose, Ndidzachitira chifundo amene ndimchitira chifundo, ndipo ndidzakhala ndi chisoni kwa iye amene ndikhala naye chisoni.
16
Chotero sichifuma kwa munthu amene afuna, kapena kwa iye amene athamanga, koma kwa Mulungu amene achitira chifundo.
17
Pakuti lembo linena kwa Farao, Chifukwa cha ichi, ndinakuutsa iwe, kuti ndikaonetse mwa iwe mphamvu yanga, ndi kuti dzina langa likabukitsidwe pa dziko lonse lapansi.
18
Chotero Iye achitira chifundo amene Iye afuna, ndipo amene Iye afuna amuumitsa mtima.
19
Pamenepo udzanena ndine kodi, Adandaulabe bwanji? Pakuti ndani anakaniza chifuno chake?
20
Koma munthu iwe, ndiwe yani wakubwezera Mulungu mau? Kodi chinthu chopangidwa chidzanena ndi amene anachipanga, Undipangiranji ine chotero?
21
Kodi kapena woumba mbiya sakutha kuchita zake padothi, kuumba ndi nchinchi yomweyo chotengera chimodzi chaulemu ndi china chamanyazi?
22
Ndipo titani ngati Mulungu, pofuna Iye kuonetsa mkwiyo wake, ndi kudziwitsa mphamvu yake, analekerera ndi chilekerero chambiri zotengera za mkwiyo zokonzekera chionongeko?
23
Ndi kuti Iye akadziwitse ulemerero wake waukulu pa zotengera zachifundo, zimene Iye anazikonzeratu kuulemerero,
24
ndi ife amenenso Iye anatiitana, si a mwa Ayuda okhaokha, komanso a mwa anthu amitundu?
25
Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhala anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.
26
Ndipo kudzali, kuti pamalo pamenepo kunanenedwa kwa iwo, Simuli anthu anga ai, pomwepo iwo adzatchedwa ana a Mulungu wamoyo.
27
Ndipo Yesaya afuula za Israele, kuti, Ungakhale unyinji wa ana a Israele ukhala monga mchenga wa kunyanja, chotsalira ndicho chidzapulumuka.
28
Pakuti Ambuye adzachita mau ake pa dziko lapansi, kuwatsiriza mwachidule.
29
Ndipo monga Yesaya anati kale, Ngati Ambuye wa makamu a kumwamba sanatisiyira ife mbeu, tikadakhala monga Sodomu, ndipo tikadafanana ndi Gomora.
30
Chifukwa chake tidzatani? Kuti amitundu amene sanatsata chilungamo, anafikira chilungamo, ndicho chilungamo cha chikhulupiriro;
31
koma Israele, potsata lamulo la chilungamo, sanafikila lamulolo.
32
Chifukwa chanji? Chifukwa kuti sanachitsata ndi chikhulupiriro, koma monga ngati ndi ntchito. Anakhumudwa pa mwala wokhumudwitsa;
33
monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika m'Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16