bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Romans 8
Romans 8
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 9 →
1
Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.
2
Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.
3
Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;
4
kuti choikika chake cha chilamulo chikakwaniridwe mwa ife, amene sitiyendayenda monga mwa thupi, koma monga mwa mzimu.
5
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu:
6
pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
7
Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.
8
Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.
9
Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.
10
Ndipo ngati Khristu akhala mwa inu, thupilo ndithu lili lakufa chifukwa cha uchimo; koma mzimu uli wamoyo chifukwa cha chilungamo.
11
Koma ngati Mzimu wa Iye amene adaukitsa Yesu kwa akufa akhalabe mwa inu, Iye amene adaukitsa Khristu Yesu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu akufa, mwa Mzimu wake wakukhala mwa inu.
12
Chifukwa chake, abale, ife tili amangawa si ake a thupi ai, kukhala ndi moyo monga mwa thupi;
13
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.
14
Pakuti onse amene atsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu, amenewo ali ana a Mulungu.
15
Pakuti inu simunalandira mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!
16
Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu;
17
ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Khristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi Iye.
18
Pakuti ndiyesa kuti masauko a nyengo yatsopano sayenera kulinganizidwa ndi ulemerero umene udzaonetsedwa kwa ife.
19
Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu.
20
Pakuti cholengedwacho chagonjetsedwa kuutsiru, chosafuna mwini, koma chifukwa cha Iye amene anachigonjetsa, ndi chiyembekezo
21
kuti cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.
22
Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m'zowawa pamodzi kufikira tsopano.
23
Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tili nazo zoundukula za Mzimu, inde ifenso tibuula m'kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu.
24
Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo; koma chiyembekezo chimene chioneka si chili chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya?
25
Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.
26
Ndipo momwemonso Mzimu athandiza kufooka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka;
27
ndipo Iye amene asanthula m'mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.
28
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
29
Chifukwa kuti iwo amene Iye anawadziwiratu, iwowa anawalamuliratu afanizidwe ndi chifaniziro cha Mwana wake, kuti Iye akakhale mwana woyamba wa abale ambiri;
30
ndipo amene Iye anawalamuliratu, iwo anawaitananso; ndimo iwo amene Iye anawaitana, iwowa anawayesanso olungama; ndi iwo amene Iye anawayesa olungama, iwowa anawapatsanso ulemerero.
31
Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?
32
Iye amene sanatimana Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?
33
Ndani adzaneneza osankhidwa a Mulungu? Mulungu ndiye amene awayesa olungama;
34
ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndiye amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso pa dzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.
35
Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?
36
Monganso kwalembedwa, Chifukwa cha Inu tilikuphedwa dzuwa lonse; tinayesedwa monga nkhosa zakupha.
37
Koma m'zonsezi, ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda.
38
Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,
39
ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16