bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Romans 4
Romans 4
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
1
Ndipo tsono tidzanena kuti Abrahamu, kholo lathu monga mwa thupi, analandira chiyani?
2
Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai.
3
Pakuti lembo litani? Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo chinawerengedwa kwa iye chilungamo.
4
Ndipo kwa iye amene agwira ntchito, mphotho siiwerengedwa ya chisomo koma ya mangawa.
5
Koma kwa iye amene sachita, koma akhulupirira Iye amene ayesa osapembedza ngati olungama, chikhulupiriro chake chiwerengedwa chilungamo.
6
Monganso Davide anena za mdalitso wake wa munthu, amene Mulungu amwerengera chilungamo chopanda ntchito,
7
ndi kuti, Odala iwo amene akhululukidwa kusaweruzika kwao, nakwiriridwa machimo ao.
8
Wodala munthu amene Mulungu samwerengera uchimo.
9
Mdalitso umenewu tsono uli kwa odulidwa kodi, kapena kwa osadulidwa omwe? Pakuti timati, Chikhulupiriro chake chinawerengedwa kwa Abrahamu chilungamo.
10
Tsono chinawerengedwa bwanji? M'mene iye anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Si wodulidwa ai, koma wosadulidwa;
11
iye ndipo analandira chizindikiro cha mdulidwe, ndicho chosindikiza chilungamo cha chikhulupiriro, chomwe iye anali nacho asanadulidwe; kuti kotero iye akhale kholo la onse akukhulupirira, angakhale iwo sanadulidwa, kuti chilungamo chiwerengedwe kwa iwonso;
12
ndiponso kholo la mdulidwe wa iwo amene siali a mdulidwe okha, koma wa iwo amene atsata mayendedwe a chikhulupiriro chija cha kholo lathu Abrahamu, chimene iye anali nacho asanadulidwe.
13
Pakuti lonjezo lakuti iye adzakhala wolowa nyumba wa dziko lapansi silinapatsidwa kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake mwa lamulo, koma mwa chilungamo cha chikhulupiriro.
14
Pakuti ngati iwo a lamulo akhala olowa nyumba, pamenepo chikhulupiriro chayesedwa chabe, ndimo lonjezo layesedwa lopanda pake;
15
pakuti chilamulo chichitira mkwiyo; koma pamene palibe lamulo, pamenepo palibe kulakwa.
16
Chifukwa chake chilungamo chichokera m'chikhulupiriro, kuti chikhale monga mwa chisomo; kuti lonjezo likhale lokhazikika kwa mbeu zonse; si kwa iwo a chilamulo okhaokha, koma kwa iwonso a chikhulupiriro cha Abrahamu; ndiye kholo la ife tonse;
17
monga kwalembedwa: Ndinakukhazika iwe kholo la mitundu yambiri ya anthu pamaso pa Mulungu amene iye anamkhulupirira, amene apatsa akufa moyo, ndi kuitana zinthu zoti palibe, monga ngati zilipo.
18
Amene anakhulupirira nayembekeza zosayembekezeka, kuti iye akakhale kholo la mitundu yambiri ya anthu, monga mwa chonenedwachi, Mbeu yako idzakhala yotere.
19
Ndipo iye osafooka m'chikhulupiriro sanalabadira thupi lake, ndilo longa ngati lakufa pamenepo, (pokhala iye ngati zaka makumi khumi), ndi mimba ya Sara idaumanso;
20
ndipo poyang'anira lonjezo la Mulungu sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, koma analimbika m'chikhulupiriro, napatsa Mulungu ulemu,
21
nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye analonjeza, anali nayonso mphamvu yakuchichita.
22
Chifukwa chake ichi chinawerengedwa kwa iye chilungamo.
23
Ndipo ichi sichinalembedwa chifukwa cha iye yekhayekha, kuti chidawerengedwa kwa iye;
24
koma chifukwa cha ifenso, kwa ife amene chidzawerengedwa kwa ife amene tikhulupirira Iye amene anaukitsa kwa akufa Yesu Ambuye wathu,
25
amene anaperekedwa chifukwa cha zolakwa zathu, naukitsidwa chifukwa cha kutiyesa ife olungama.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16