bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezra 1
Ezra 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 2 →
1
Chaka choyamba cha ulamuliro wa Kirusi, mfumu ya ku Persiya, Chauta adachitadi zimene adaanena kudzera mwa Yeremiya. Adaika maganizo mumtima mwa Kirusi, ndipo iye adalengeza m'dziko lake lonse ndi mau apakamwa, mpakanso ochita kulemba. Adati,
2
“Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu Wakumwamba, wandipatsa ine maiko onse a pa dziko lonse lapansi, ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda.
3
Tsono inu nonse amene muli akeake, Mulungu wanuyo akhale nanu. Aliyense mwa inu apite ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda, kuti akamange Nyumba ya Chauta, Mulungu wa Israele. Iyeyo ndiye Mulungu amene amampembedza ku Yerusalemu.
4
Motero kulikonse kumene anthu otsalawo amakhala, athandizidwe ndi eni dzikolo. Aŵapatse siliva ndi golide, katundu ndi ziŵeto, ndi zopereka zaufulu zoti akapereke ku Nyumba ya Mulungu, imene ili ku Yerusalemu.’ ”
5
Choncho atsogoleri amabanja a fuko la Yuda ndi la Benjamini, ndiponso ansembe ndi Alevi, adayamba kukonzeka, aliyense amene mumtima mwake Mulungu adamupatsa maganizo oti apite kukamanganso Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu.
6
Onse oyandikana nawo adaŵathandiza poŵapatsa ziŵiya zasiliva, golide, katundu, ziŵeto ndiponso mphatso zamtengowapatali, kuphatikizapo zopereka zija zimene ankazipereka mwaufulu.
7
Nayenso mfumu Kirusi adatulutsa ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta zimene Nebukadinezara adaazitenga kuzichotsa ku Yerusalemu, kudzaziika m'nyumba ya milungu yake.
8
Kirusi, mfumu ya ku Persiya, idazitulutsa zimenezi nkuzipereka kwa Metiredati, msungachuma wake, amene adaziŵerenga pamaso pa Sesibazara, nduna yaikulu ya ku dziko la Yuda.
9
Chiŵerengero chake chinali chotere: Mabeseni agolide 30 a zopereka, mabeseni asiliva 1,000 a zopereka, zofukizira 29,
10
timikhate tagolide 30, timikhate tasiliva 2,410, ndi ziŵiya zinanso 1,000.
11
Ziŵiya zagolide ndi zasiliva zonse pamodzi zidakwanira 5,400. Zonsezi ndizo zimene Sesibazara adabwera nazo pamene akuukapolo aja ankabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babiloni.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10