bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezra 10
Ezra 10
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
1
Pamene Ezara ankapemphera ndi kulapa, alikulira ndipo atadzigwetsa pansi ku Nyumba ya Mulungu, chinamtindi cha anthu chidabwera kwa iye kudzasonkhana. Panali amuna, akazi ndi ana, kuchokera m'dziko lonse la Israele, ndipo ankalira koopsa.
2
Tsono Sekaniya, mwana wa Yehiyele, wa fuko la Elamu, adauza Ezara kuti, “Ife takhala osakhulupirika kwa Mulungu wathu, ndipo takhala tikukwatira akazi achilendo a mitundu ya m'maiko akunoŵa. Koma ngakhale zili choncho, chikhulupiriro chilipobe pakati pa Aisraele.
3
Tiyeni tsono tichite naye chipangano Mulungu wathu, kuti ifeyo tilekane nawo akazi ameneŵa pamodzi ndi ana ao, potsata uphungu wa inu mbuyanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Ndipo tidzazichitadi potsata malamulowo.
4
Ndiye inu dzukani, imeneyi ndi ntchito yanu, ndipo ife tili nanu. Valani dzilimbe ndipo muigwire ntchitoyo.”
5
Choncho Ezara adanyamuka ndipo adalumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraele onse, kuti adzachitedi monga m'mene Sekaniya adaanenera. Tsono onsewo adalumbira.
6
Pambuyo pake Ezara adachokako ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu, kumene adakachezera usikuwo. Sadadye buledi kapena kumwa madzi. Nthaŵi yonseyo adakhalira kulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo aja.
7
Tsono anthu adalengeza m'dziko lonse la Yuda ndi mu mzinda wa Yerusalemu, kwa onse ochokera ku ukapolo aja, kuti asonkhane ku Yerusalemu.
8
Adanena kuti, “Wina aliyense akapanda kufika asanathe masiku atatu, ndiye kuti potsata lamulo la atsogoleri ndi la akulu, adzayenera kumlanda katundu wake yense, ndipo adzachotsedwe m'gulu la anthu obwerako ku ukapolo aja.”
9
Choncho anthu onse a m'dziko la Yuda ndi a m'dziko la Benjamini adasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wachisanu ndi chinai. Ndipo anthu onse adakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu, ali njenjenje chifukwa cha nkhani imeneyi ndiponso chifukwa cha mvula yambiri imene inkagwa.
10
Tsono wansembe Ezara adaimirira nati, “Mudachimwa pomakwatira akazi achikunja, ndipo mudaonjezera tchimo la Israele.
11
Lapani tsopano kwa Chauta, Mulungu wa makolo anu, ndipo muchite zimene Iye akufuna. Dzichotseni pakati pa mitundu ya anthu a m'maiko enaŵa, ndi pa akazi achilendowo.”
12
Chitamva mau amenewo, chinantindi chonse chapamsonkhanopo chidayankha mokweza mau kuti, “Ndi chonchodi, tiyenera kuchitadi monga mwaneneramo.
13
Koma anthu ali panoŵa ngambiri, ndipo mvula ikugwa kwamphamvu, sitingathe kukaima pa mtetete. Chinanso nchakuti ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena masiku aŵiri, pakuti tidachimwa kwambiri pa nkhani imeneyi.
14
Tsono atsogoleri athu aimirire m'malo mwa msonkhano wonse. Anthu onse a m'mizinda yathu amene adakwatira akazi achilendo abwere pa nthaŵi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akulu ndi aweruzi a mzinda uliwonse. Motero mkwiyo woopsa wa Mulungu wathu pa nkhani imeneyi udzachoka.”
15
Yonatani yekha, mwana wa Asahele, ndiponso Yahazeiya, mwana wa Tikiwa, ndi amene adatsutsapo pa zimenezi, ndipo Mesulamu pamodzi ndi Mlevi Sabetai, adaŵavomereza.
16
Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja, adachitadi momwemo. Wansembe Ezara adasankha anthu, akulu a mabanja potsata mafuko ao, aliyense kuchita kumlemba dzina. Pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, adayambapo kuifufuza nkhani imeneyi.
17
Ndipo pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, anali atathana nawo anthu amene adaakwatira akazi achilendo aja.
18
Nawu mndandanda wa ansembe amene adaakwatira akazi achilendo: Pa banja la Yesuwa ndi abale ake, ana a Yozadaki, panali aŵa: Maaseiya, Eliyezere, Yaribu ndi Gedaliya.
19
Iwo adatsimikiza zochotsa akazi ao, ndipo adapereka nkhosa yamphongo yopepesera machimo ao.
20
Pa banja la Imara panali Hanani ndi Zebadiya.
21
Pa banja la Harimu panali Maaseiya, Eliya, Semaya, Yehiyele ndi Uziya.
22
Pa banja la Pasuri panali Eliyoenai, Maaseiya, Ismaele, Netanele, Yozabadi ndi Elasa.
23
Pakati pa Alevi panali aŵa: Yosabadi, Simei, Kelaya (amene ankatchedwanso Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliyezere.
24
Pakati pa oimba nyimbo, panali Eliyasibu. Pakati pa alonda a ku Nyumba ya Mulungu panali Salumu, Telemu ndi Uri.
25
Pakati pa Israele: a fuko la Parosi anali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eleazara, Hasabiya ndi Benaya.
26
A fuko la Elamu anali Mataniya, Zekariya, Yehiyele, Abidi, Yeremoti ndi Eliya.
27
A fuko la Zatu anali Eliyoenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi, ndi Aziza.
28
A fuko la Bebai anali Yehohanani, Hananiya, Zabibai ndi Atilai.
29
A fuko la Bani anali Mesulamu, Malaki, Adaya, Yasubu, Seyala ndi Yeremoti.
30
A fuko la Pahatimowabu anali Adina, Kelali, Benaya, Maaseiya, Mataniya, Bezalele, Binuyi ndi Manase.
31
A fuko la Harimu anali Eliyezere, Isiya, Malikiya, Semaya, Simeoni
32
Benjamini, Maluki ndi Semariya.
33
A fuko la Hasumu anali Matenai, Matata, Zebadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simei.
34
A fuko la Bani anali Maadai, Amuramu, Uwele,
35
Benaya, Bedeiya, Keluhu,
36
Vaniya, Meremoti, Eliyasibu,
37
Mataniya, Metenai, ndi Yasu.
38
A fuko la Binuyi anali Simei,
39
Selemiya, Natani, Adaya,
40
Makinadebai, Sasai, Sarai,
41
Azarele, Seremiya, Semariya,
42
Salumu, Amariya ndi Yosefe.
43
A fuko la Nebo anali Yeiyele, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yowele ndi Benaya.
44
Onseŵa adaakwatira akazi achilendo. Tsono adaŵasudzula akaziwo pamodzi ndi ana ao omwe.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10