bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezra 2
Ezra 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 3 →
1
Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaaŵagwira nkupita nawo ku ukapolo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
2
Adabwera pamodzi ndi atsogoleri aŵa: Zerubabele, Yesuwa, Nehemiya, Seraya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana. Nachi chiŵerengero cha anthu aamuna a Aisraele:
3
A banja la Parosi, 2,172.
4
A banja la Sefatiya, 372.
5
A banja la Ara, 775.
6
A banja la Pahatimowabu, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa ndi Yowabu, 2,812.
7
A banja la Elamu, 1,254.
8
A banja la Zatu, 945.
9
A banja la Zakai, 760.
10
A banja la Bani, 642.
11
A banja la Bebai, 623.
12
A banja la Azigadi, 1,222.
13
A banja la Adonikamu, 666.
14
A banja la Bigivai, 2,056.
15
A banja la Adini, 454.
16
A banja la Atere, ndiye kuti la Hezekiya, 98.
17
A banja la Bezai, 323.
18
A banja la Yora, 112.
19
A banja la Hasumu, 223.
20
A banja la Gibara, 95.
21
Amuna a ku Betelehemu, 123.
22
Amuna a ku Netofa, 56.
23
Amuna a ku Anatoti, 128.
24
A banja la Azimaveti, 42.
25
A banja la Kiriyati-Arimu, Kefira ndi Beeroti, 743.
26
A banja la Rama ndi Geba, 621.
27
Amuna a ku Mikimasi, 122.
28
Amuna a ku Betele ndi ku Ai, 223.
29
A banja la Nebo, 42.
30
A banja la Magabisi, 156.
31
A banja la Elamu wina, 1,254.
32
A banja la Harimu, 320.
33
A banja la Lodi, Hadidi ndi Ono, 725.
34
A banja la Yeriko, 345.
35
A banja la Sena, 3,630.
36
Ansembe anali aŵa: a banja la Yedaya, ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa, 973.
37
A banja la Imeri, 1,052.
38
A banja la Pasuri, 1,247.
39
A banja la Harimu, 1,017.
40
Alevi anali aŵa: a banja la Yesuwa ndi la Kadimiyele, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya, 74.
41
Oimba nyimbo anali aŵa: a banja la Asafu, 128.
42
Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Salumu, a banja la Atere, a banja la Talimoni, a banja la Akibu, a banja la Hatita, ndi a banja la Sobai, onse pamodzi 139.
43
Antchito a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: a banja la Ziha, a banja la Hasufa, a banja la Tabaoti,
44
a banja la Kerosi, a banja la Siyaha, a banja la Padoni,
45
a banja la Lebana, a banja la Hagaba, a banja la Akubu,
46
a banja la Hagabu, a banja la Salimai, a banja la Hanani,
47
a banja la Gidele, a banja la Gahara, a banja la Reaya,
48
a banja la Rezini, a banja la Nekoda, a banja la Gazamu,
49
a banja la Uza, a banja la Paseya, a banja la Bosai,
50
a banja la Asina, a banja la Meunimu, a banja la Nefisimu,
51
a banja la Bakibuki, a banja la Hakufa, a banja la Harihuri,
52
a banja la Baziluti, a banja la Mehida, a banja la Harisa,
53
a banja la Barikosi, a banja la Sisera, a banja la Tema,
54
a banja la Neziya ndi a banja la Hatifa.
55
Mabanja a antchito ake a Solomoni anali aŵa: a banja la Sotai, a banja la Hasopereti, a banja la Peruda,
56
a banja la Yaala, a banja la Darikoni, a banja la Gidele,
57
a banja la Sefatiya, a banja la Hatili, a banja la Pokereti-Hazebaimu ndi a banja la Ami.
58
Antchito onse a ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo zidzukulu za antchito a Solomoni, onse analipo 392 pamodzi.
59
Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai.
60
A banja la Delaya, a banja la Tobiya ndi a banja la Nekoda, 642.
61
Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Habaya, a banja la Hakozi ndi a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).
62
Iwoŵa adafunafuna maina ao m'buku lolongosola kaundula wa mafuko ao, koma maina ao sadapezekemo. Choncho adaŵachotsa pa unsembe, naŵaŵerenga kuti ngodetsedwa pa chipembedzo.
63
Bwanamkubwa adaŵauza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya choperekedwa kwa Mulungu, mpaka wansembe wodziŵa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu atapezeka.
64
Chiŵerengero cha anthu onse obwerako ku ukapolo aja chinali 42,360.
65
Kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito ao aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Anali nawonso anthu oimba nyimbo, amuna ndi akazi omwe, okwanira 200.
66
Akavalo ao analipo 736, nyulu zao zinalipo 245,
67
ngamira zao zinalipo 435 ndipo abulu ao analipo 6,720.
68
Pamene adabwera ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zaufulu, kuperekera Nyumba ya Mulungu, kuti imangidwenso pamalo pake pakale.
69
Adapereka kwa msungachuma wa ntchitoyo molingana ndi chuma chao, golide wa makilogaramu 500, ndi siliva wa makilogaramu 2,800, ndiponso zovala za ansembe zokwanira 100.
70
Ansembe, Alevi ndi anthu ena ankakhala mu mzinda wa Yerusalemu ndi m'midzi yake yozungulira. Anthu oimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso Aisraele ena onse, ankakhala m'midzi ya makolo ao.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10