bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ezra 4
Ezra 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 5 →
1
Adani a Yuda ndi a Benjamini adaamva kuti anthu obwerako ku ukapolo aja akumangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Aisraele.
2
Ndiye adadza kwa Zerubabele ndi kwa atsogoleri a mabanja, naŵauza kuti, “Mutilole kuti timange nawo, pakuti ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthaŵi ya Ezaradoni, mfumu ya ku Asiriya, amene adatifikitsa kuno.”
3
Koma Zerubabele, Yesuwa, ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a m'dziko la Israele adaŵayankha kuti, “Sitikusoŵa chithandizo chanu pa ntchito iyi yomangira Nyumba Mulungu wathu. Koma ife tokha tidzammangira Nyumba Chauta, Mulungu wa Israele, monga mfumu Kirusi, mfumu ya ku Persiya, adatilamula.”
4
Atamva zimenezi anthu a m'dzikomo adayamba kutayitsa mtima Ayuda, ndi kuŵachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo.
5
Adalemba akuluakulu ena kuti alepheretse cholinga chao cha pa ntchitoyo pa nthaŵi yonse ya Kirusi, mfumu ya ku Persiya, ngakhalenso mpaka pamene Dariusi, mfumu ya ku Persiya ankalamulira dzikolo.
6
Pamene mfumu Ahasuwero adayamba kulamulira dziko, adani aja adalemba kalata yoneneza nzika zija za ku Yuda ndi za ku Yerusalemu.
7
Chimodzimodzinso pa nthaŵi ya Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Persiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabiyele ndi anzao ena, adalemba inanso kalata kwa Arita-kisereksesiyo. Kalatayo adailemba m'Chiaramu, ndipo poiŵerenga ankachita kutanthauzira.
8
Kenaka Rehumu Bwanamkubwa ndi Simisai mlembi wake, nawonso adalemba yao kalata kwa mfumu Arita-kisereksesi yoneneza anthu a ku Yerusalemu. Adalemba motere:
9
“Kalatayi ikuchokera kwa Rehumu bwanamkubwa, mlembi Simisai ndi anzao aŵa: aweruzi, nduna ndi akuluakulu ena, anthu a ku Persiya ndi ku Ereki, ku Babiloniya, ndi ku Susa, m'dziko la Elami.
10
Enanso ndi mitundu ina imene Osinapara, wamkulu ndi womveka uja, adaisamutsa ndi kuikhazika m'mizinda ya Samariya ndi kwinanso m'madera a m'chigawo chimene chili Patsidya pa Yufurate.”
11
Mau ake a m'kalata imene adatumizayo ndi aŵa: “Zikomo, amfumu Arita-kisereksesi, ife atumiki anu, a m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, poyamba tikukupatsani moni.
12
Amfumu, tikuti mudziŵeko kuti Ayuda omwe adabwera kuno kuchokera kwanuko, apita ku Yerusalemu. Akumanganso mzinda wopanduka ndi woipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonza maziko.
13
Tsonotu amfumu, mudziŵe kuti akaumanganso mzinda umenewu ndi kumaliza kumanga makoma ake, ndiye kuti anthu aja adzaleka kukhoma msonkho ndi kupereka kasitomo kapena msonkho wa kanthu kena kalikonse, ndipo chuma choloŵa m'thumba la mfumu chidzachepa.
14
Tsono popeza kuti ife ndife akadyere kwa mfumu, si bwino kuti tizingopenya zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nchifukwa chake tikutumiza mau kwa inu mfumu kuti mudziŵe zonse.
15
Ndi bwino kuti pachitike kafukufuku m'buku la mbiri yakale ya makolo anu. M'buku lazakalemo mudzapeza ndi kuŵerengamo kuti mzinda umenewo ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zam'madera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuchita zoukira ulamuliro uliwonse. Nchifukwa chake mzinda umene uja adausandutsa bwinja.
16
Tikukudziŵitsani inu amfumu kuti ngati mzinda umenewu aumanganso ndi kutsirizanso makoma ake, ndiye kuti inuyo simudzatha kumalamulirabe m'chigawo cha Patsidya pa Yufuratecho.”
17
Tsono mfumuyo idayankha kalatayo motere, “Bwanamkubwa Rehumu ndi mlembi Simisai, ndi anzanu ena amene akukhala ku Samariya ndi m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, ndikuti moni.
18
Kalata imene mudatumiza, aiŵerenga pamaso panga momveka bwino.
19
Ine nditalamula kuti afufuzefufuze nkhaniyi, kwapezekadi kuti mzinda umenewo udaaukira mafumu kale, ndipo kuti zaupandu ndi zoukira zinkachitikadi m'menemo.
20
Mafumu amphamvu adakhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonsecho cha Patsidya pa Yufurate, namalandira kasitomo ndi msonkho pa kanthu kena kalikonse.
21
Tsono inu mulembe lamulo loŵaletsa anthu amenewo kuti asamangenso mzinda umenewo, mpaka ine nditaloleza.
22
Ndithu zimenezi musachedwetse. Nanga ndingalole bwanji kuti zoononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?”
23
Kalata ya mfumu Arita-kisereksesiyo ataiŵerenga pamaso pa Rehumu ndi mlembi Simisai ndi anzao, iwowo adapita msangamsanga ku Yerusalemu, nakaŵaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirize ntchito yao.
24
Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu idalekeka mpaka chaka chachiŵiri cha ufumu wa Dariusi, mfumu ya ku Persiya.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10