bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hebrews 1
Hebrews 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
1
Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri.
2
Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake.
3
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
4
Mwana wa Mulunguyo ngwoposa angelo, monga momwe dzina limene Mulungu adampatsa limaposera dzina la angelo.
5
Nchifukwa chake nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.” Mulungu sadakambepo za mngelo aliyense kuti, “Ine ndidzakhala bambo wake, iye adzakhala mwana wanga.”
6
Koma pamene ankatuma Mwana wake wachisamba pansi pano, Mulungu adati, “Angelo onse a Mulungu azimpembedza.”
7
Ndipo za angelo Mulungu adati, “Mulungu amasandutsa angelo ake mphepo, atumiki ake amaŵasandutsa malaŵi a moto.”
8
Koma za Mwana wake adati, “Inu Mulungu, mpando wanu wachifumu udzakhala mpaka muyaya, chilungamo ndicho chili ngati ndodo yachifumu mu ulamuliro wanu.
9
Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama. Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe, kupambana anzanu ena onse.”
10
Adatinso, “Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi pachiyambi pomwe, zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu.
11
Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire. Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala.
12
Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.”
13
Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.”
14
Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso?
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13