bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hebrews 8
Hebrews 8
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 9 →
1
Mfundo yeniyeni pa zimene tikunenazi ndi iyi: tili naye wotere Mkulu wa ansembe onse, amene akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu Waulemerero Kumwamba.
2
Iye akutumikira m'Malo Opatulika am'katikati, ndiye kuti m'chihema chenicheni chimene adachimanga ndi Ambuye osati munthu ai.
3
Paja mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka mphatso ndi nsembe kwa Mulungu. Motero nkofunika kuti wathunso mkulu wa ansembe onse akhale nkanthu koti apereke.
4
Iyeyu akadakhala pa dziko lapansi, sibwenzi ali wansembe konse, popeza kuti alipo kale ansembe amene amapereka mphatso potsata Malamulo a Mose.
5
Ntchito za chipembedzo zimene iwo amachita, zili ngati chithunzi chongofanizira zenizeni za Kumwamba. Paja zidaateronso ndi Mose: pamene iye adaati amange chihema, Mulungu adaamlangiza kuti, “Upangetu zonse molingana ndi chitsanzo chimene ndidaakuwonetsa paphiri paja.”
6
Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija.
7
Chipangano choyamba chija chikadakhala changwiro, sipakadafunikanso china m'malo mwake.
8
Koma Mulungu adadzudzula anthu ake ndi mau aŵa akuti, “Masiku akubwera, pamene ndidzachita chipangano chatsopano ndi fuko la Israele, ndiponso ndi fuko la Yuda.
9
Sichidzakhala chonga chipangano chimene ndidaachita ndi makolo ao tsiku limene ndidaachita kuŵagwira pa dzanja kuti ndiŵatulutse m'dziko la Ejipito. Chifukwa iwo sadasunge chipangano changa chija, nanenso sindidaŵasamale”, akutero Ambuye.
10
“Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga.
11
Sipadzafunikanso kuti wina aliyense aphunzitse mnzake, kapena kuti wina aliyense auze mbale wake kuti, ‘Udziŵe Ambuye’. Pakuti onse adzandidziŵa, kuyambira wamng'ono mpaka wamkulu.
12
Mwachifundo ndidzaŵakhululukira zochimwa zao, sindidzakumbukiranso machimo ao.”
13
Pakunena mau oti, “Chipangano chatsopano”. Mulungu akunena kuti chipangano choyamba nchotha ntchito. Paja chinthu chimene chayamba kutha ntchito nkumakalamba, ndiye kuti chili pafupi kuzimirira.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13