bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hebrews 5
Hebrews 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 6 →
1
Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa pakati pa anthu, namuika kuti aziŵaimirira pamaso pa Mulungu. Ntchito yake nkupereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo.
2
Popeza kuti iye yemweyo ali ndi zofooka zambiri, ndiye kuti angathe kuŵalezera mtima amene ali opanda nzeru ndi osokera.
3
Nchifukwa chake aumirizidwa kumapereka nsembe chifukwa cha machimo a iye yemwe, ndiponso machimo a anthu ena.
4
Palibe munthu amadzitengera yekha ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma amachita kuitanidwa ndi Mulungu, monga momwe adaaitanidwira Aroni.
5
Momwemonso Khristu sadadzikweze yekha ku ulemu wokhala mkulu wa ansembe onse, koma Mulungu ndiye adachita kumuuza kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga, Ine lero ndakubala.”
6
Penanso Mulungu adati, “Ndiwe wansembe mpaka muyaya, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.”
7
Yesu, pa nthaŵi imene anali munthu pansi pano, mofuula ndi molira misozi, adapereka mapemphero ndi madandaulo kwa Mulungu, amene anali nazo mphamvu zompulumutsa ku imfa. Ndiye popeza kuti Yesu adaadzipereka modzichepetsa, Mulungu adamvera mapemphero ake.
8
Motero Yesu, ngakhale anali Mwana wa Mulungu, adaphunzira kumvera pakumva zoŵaŵa.
9
Atasanduka wangwiro kotheratu, adakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye,
10
ndipo Mulungu adamtchula mkulu wa ansembe onse, unsembe wake wonga uja wa Melkizedeki.
11
Tili ndi zambiri zoti nkunena pa zimenezi, koma nzovuta kufotokoza kwake, popeza kuti mwasanduka ouma mitu.
12
Lija nkale mukadayenera kukhala ophunzitsa anzanu, komabe nkofunika kuti wina akuphunzitseninso maphunziro oyamba enieni a mau a Mulungu. Nkofunikanso kukumwetsani mkaka, m'malo mwa kukupatsani chakudya cholimba.
13
Ngati wina aliyense angomwa mkaka, ndiye kuti akali mwana wakhanda, sangathe kutsata chiphunzitso chofotokoza za chilungamo.
14
Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima. Pakugwiritsa ntchito nzeru zao, iwoŵa adadzizoloŵeza kusiyanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13