bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Hebrews 3
Hebrews 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 4 →
1
Abale, ndinu oyera ake a Mulungu, inuyo adakuitanani kuti nanunso mukhale ndi moyo wakumwamba. Nchifukwa chake muzisinkhasinkha za Yesu, mtumwi wa Mulungu, ndiponso Mkulu wa ansembe onse wa chikhulupiriro chimene timavomereza.
2
Paja Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene adampatsa udindowo, monga momwe Mosenso anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu.
3
Munthu womanga nyumba amalandira ulemu woposa ulemerero wa nyumbayo. Momwemonso Yesu ngwoyenera kulandira ulemerero woposa ulemerero wa Mose.
4
Nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wakutiwakuti, koma amene adapanga zonse, ndi Mulungu.
5
Mose anali wokhulupirika m'nyumba yonse ya Mulungu ngati wantchito chabe, kuti achitire umboni zimene Mulungu analikudzanena m'tsogolo mwake.
6
Koma Khristu anali wokhulupirika m'nyumba ya Mulungu ngati mwana wolamulira pa zonse za m'nyumba mwakemo. Ndipo nyumba yakeyo ndife, ngati tiika mphamvu pa kulimba mtima ndi kunyadira zimene tikuziyembekeza.
7
Nchifukwa chake tsono, monga Mzimu Woyera akunenera, “Lero lino mukamva mau a Mulungu,
8
musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira pomuukira Mulungu, tsiku la kumuyesa m'chipululu muja.
9
Mulungu akuti, Pamene paja, makolo anu adaandiputa pakundiyesa, ndipo adaona zimene ndidaŵachita pa zaka makumi anai.
10
Tsono ndidaukwiyira mbadwowo, ndipo ndidati, ‘Nthaŵi zonse amasokera mumtima mwao, sanaphunzirebe njira zanga.’
11
Motero ndili wokwiya ndidalumbira kuti, ‘Sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera.’ ”
12
Abale, mchenjere, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woipa ndi wosakhulupirira, womlekanitsa ndi Mulungu wamoyo.
13
Kwenikweni muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku ikadalipo nthaŵi, imene m'mau a Mulungu imatchedwa kuti, “Lero”. Muzichita zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense mwa inu angaumitsidwe mtima ndi chinyengo cha uchimo.
14
Paja timasanduka anzake a Khristu, malinga tikasunga kwenikweni mpaka potsiriza kulimba mtima kumene tinali nako poyamba.
15
Paja Malembo akuti, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.”
16
Nanga amene adaamva mau ake a Mulungu namuukira, ndani? Ndi onse aja amene Mose adaaŵatsogolera nkuŵatulutsa m'dziko la Ejipito.
17
Nanga amene Mulungu adaaŵakwiyira zaka makumi anai, ndani? Ndi anthu amene adaachimwa aja, mitembo yao nkutsalira m'chipululu.
18
Nanga Mulungu ankanena za yani pamene adaati, “Ndikulumbira kuti ameneŵa sadzaloŵa konse mu mpumulo umene ndidaŵakonzera?” Pajatu ankanena za anthu amene adaamuukira.
19
Motero tikuwona kuti anthuwo sadathe kuloŵa, chifukwa cha kusakhulupirira.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13