bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Psalms 119
Psalms 119
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 118
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 67
Chapter 68
Chapter 69
Chapter 70
Chapter 71
Chapter 72
Chapter 73
Chapter 74
Chapter 75
Chapter 76
Chapter 77
Chapter 78
Chapter 79
Chapter 80
Chapter 81
Chapter 82
Chapter 83
Chapter 84
Chapter 85
Chapter 86
Chapter 87
Chapter 88
Chapter 89
Chapter 90
Chapter 91
Chapter 92
Chapter 93
Chapter 94
Chapter 95
Chapter 96
Chapter 97
Chapter 98
Chapter 99
Chapter 100
Chapter 101
Chapter 102
Chapter 103
Chapter 104
Chapter 105
Chapter 106
Chapter 107
Chapter 108
Chapter 109
Chapter 110
Chapter 111
Chapter 112
Chapter 113
Chapter 114
Chapter 115
Chapter 116
Chapter 117
Chapter 118
Chapter 119
Chapter 120
Chapter 121
Chapter 122
Chapter 123
Chapter 124
Chapter 125
Chapter 126
Chapter 127
Chapter 128
Chapter 129
Chapter 130
Chapter 131
Chapter 132
Chapter 133
Chapter 134
Chapter 135
Chapter 136
Chapter 137
Chapter 138
Chapter 139
Chapter 140
Chapter 141
Chapter 142
Chapter 143
Chapter 144
Chapter 145
Chapter 146
Chapter 147
Chapter 148
Chapter 149
Chapter 150
Chapter 120 →
1
Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta.
2
Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
3
amene sachita zolakwa, koma amayenda m'njira za Chauta.
4
Inu Chauta, mwapereka malamulo anu ndipo mwalamula kuti atsatidwe kwathunthu.
5
Ndikadakonda kuti njira zanga zikhale zokhulupirika, pakumvera malamulo anu.
6
Tsono anthu sadzandichititsa manyazi, ndikatsata malamulo anu onse.
7
Ndidzakutamandani ndikuchita zoyenera, ndikaphunzira malangizo anu olungama.
8
Ndidzatsata malamulo anu, musandisiye konse ndekha.
9
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
10
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.
11
Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.
12
Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu.
13
Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu.
14
Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.
15
Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu.
16
Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala.
17
Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu.
18
Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu.
19
Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu.
20
Mtima wanga wafooka chifukwa cholakalaka malangizo anu nthaŵi zonse.
21
Inu mumadzudzula onyada, amene ali otembereredwa, amene amasiya malamulo anu.
22
Mundichotsere zonyoza zao zondinyodola, chifukwa ndasunga malamulo anu.
23
Ngakhale mafumu andichitire upo woipa, ine mtumiki wanu ndidzasinkhasinkhabe za malamulo anu.
24
Malamulo anu amandikondwetsa, ndiwo amene amandilangiza.
25
Ndangoti thapsa m'fumbi. Bwezereni moyo monga momwe mudalonjezera.
26
Pamene ndidasimba za njira zanga, Inu mudandiyankha. Phunzitseni malamulo anu.
27
Mundidziŵitse mfundo za malamulo anu, ndipo ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zodabwitsa.
28
Ndafookeratu ndi chisoni. Limbitseni monga momwe mudalonjezera.
29
Mundichotse m'njira zondisokeza, kuti ndisayendemo. Mundikomere mtima pondiphunzitsa malamulo anu.
30
Ine ndasankhula njira yoti ndizikhala wokhulupirika, ndaika malangizo anu mumtima mwanga.
31
Ndimakangamira malamulo anu, Inu Chauta, musalole kuti anthu andichititse manyazi.
32
Ndidzatsata mokondwa njira ya malamulo anu, mukandiwonjezera nzeru.
33
Chauta, phunzitseni njira zosungira malamulo anu, ndipo ndidzazitsata mpaka kumathero.
34
Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu, ndiziŵatsata ndi mtima wanga wonse.
35
Munditsogolere kuti ndimvere malamulo anu, chifukwa ndimakondwera nawo.
36
Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.
37
Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.
38
Munditsimikizire ine mtumiki wanu chipangano chanu, chimene mumachita ndi anthu okuwopani.
39
Mundichotsere chipongwe chimene ndimachiwopa, chifukwa malangizo anu ndi abwino.
40
Onani ndikulakalaka kutsata malamulo anu. Mundipatse moyo chifukwa ndinu olungama.
41
Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, mundipulumutse monga momwe mudalonjezera.
42
Pamenepo ndidzakhala nchoŵayankha anthu ondinyodola, pakuti ndimakhulupirira mau anu.
43
Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu.
44
Ndidzatsata malamulo anu kosalekeza mpaka muyaya,
45
ndipo ndidzayenda ndi ufulu, chifukwa ndasamala malamulo anu.
46
Ndidzalankhula malamulo anu pamaso pa mafumu, ndipo anthu sadzandichititsa manyazi.
47
Inetu ndimasangalala ndi malamulo anu amene ndimaŵakonda.
48
Ndimalemekeza malamulo anu amene ndimaŵakonda, ndipo ndimasinkhasinkha za malamulowo.
49
Kumbukirani mau anu aja kwa ine mtumiki wanu, mau amene amandipatsa chikhulupiriro.
50
Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo.
51
Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu, komabe sindisiyana nawo malamulo anu.
52
Inu Chauta, ndikamalingalira malamulo anu akalekale, ndimasangalala,
53
Ndimapsa mtima kwambiri chifukwa cha anthu oipa amene amaphwanya malamulo anu.
54
Malamulo anu asanduka nyimbo yanga kulikonse kumene ndimapita.
55
Ndimakukumbukirani usiku, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu.
56
Madalitso ameneŵa andifikira ine, pakuti ndimatsata malamulo anu.
57
Inu Chauta, zanga zonse ndinu, ndikulonjeza kumvera mau anu.
58
Ndikukupemphani ndi mtima wanga wonse, mundikomere mtima molingana ndi malonjezo anu aja.
59
Ndikamalingalira njira zanga, ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu.
60
Ndimafulumira, sindizengereza kutsata malamulo anu.
61
Ngakhale anthu oipa anditchere msampha, sindiiŵala malamulo anu.
62
Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikutamandeni, chifukwa cha malangizo anu olungama.
63
Ine ndine bwenzi la anthu okuwopani, anthu otsata malamulo anu.
64
Inu Chauta, dziko lapansi nlodzaza ndi chikondi chanu chosasinthika, phunzitseni malamulo anu.
65
Inu Chauta, mwandikomera mtima mtumiki wanune, molingana ndi mau anu.
66
Patseni luntha ndi nzeru, chifukwa ndimakhulupirira malamulo anu.
67
Ndisanayambe kulangika ndinkasokera, koma tsopano ndimamvera mau anu.
68
Inu ndinu abwino, ndipo mumachita zabwino, phunzitseni malamulo anu.
69
Anthu osasamala za Mulungu amandisinjirira, komabe ndimatsata malamulo anu ndi mtima wanga wonse.
70
Anthu otere ndi opulukira, koma ine ndimakondwa ndi malamulo anu.
71
Ndi bwino kuti ndidalangidwa, kuti ndiphunzire malamulo anu.
72
Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.
73
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
74
Anthu okuwopani adzandiwona ndipo adzakondwa, popeza kuti ndakhulupirira mau anu.
75
Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.
76
Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.
77
Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo, pakuti malamulo anu amandikondwetsa.
78
Anthu osasamala za Mulungu muŵachititse manyazi, chifukwa andilakwira pondinamizira. Koma ine ndidzasinkhasinkha za malamulo anu.
79
Anthu okuwopani abwere kwa ine kuti aphunzire malamulo anu.
80
Mtima wanga ukhale wopanda choudzudzulira pa malamulo anu, kuti ndisachite manyazi.
81
Moyo wanga wafooka podikira chipulumutso chanu, ndikukhulupirira mau anu.
82
Maso anga afiira nkuyang'anira malonjezo anu. Ndimafunsa kuti, “Kodi mudzandithandiza liti?”
83
Ndasanduka ngati thumba lachikopa lokhwinyata, komabe sindiiŵala malamulo anu.
84
Kodi mtumiki wanune ndipirire mpaka liti? Kodi anthu ondizunza mudzaŵalanga liti?
85
Anthu osasamala za Mulungu, osatsata malamulo anu, andikumbira mbuna.
86
Malamulo anu onse ndi osasinthika. Anthuwo amandizunza ndi mabodza ao; thandizeni!
87
Adatsala pang'ono kundichotsa pa dziko lapansi, komabe sindidaleke kutsata malamulo anu.
88
Sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, kuti nditsate malamulo anu.
89
Inu Chauta, mau anu ngokhazikika kumwambako mpaka muyaya.
90
Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka pa mibadwo yonse. Inu mwakhazikitsa dziko, ndipo siligwedezeka.
91
Zolengedwa zikupezeka lero lino chifukwa cha kulamula kwanu, pakuti zinthu zonse zimakutumikirani.
92
Malamulo anu akadapanda kundisangalatsa, bwenzi nditafa ndi mazunzo anga.
93
Sindidzaiŵala konse malangizo anu, pakuti mwandipatsa nawo moyo.
94
Ndine wanu, pulumutseni, pakuti ndasamala malamulo anu.
95
Anthu oipa amandiŵenda kuti andiwononge, koma ine ndimalingalira za malamulo anu.
96
Ndazindikira kuti zabwino zonse zili ndi malire, koma malamulo anu alibe konse malire.
97
Ndimakonda malamulo anu kwambiri, ndimasinkhasinkha za malamulowo tsiku lonse.
98
Malamulo anu amandisandutsa wanzeru kuposa adani anga, popeza kuti malamulowo ndili nawo nthaŵi zonse.
99
Ndili ndi nzeru za kumvetsa kupambana aphunzitsi anga onse, pakuti ndimasinkhasinkha za malamulo anu.
100
Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu.
101
Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu.
102
Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa
103
mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga.
104
Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.
105
mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.
106
Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama.
107
Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja.
108
Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu.
109
Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu.
110
Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu.
111
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
112
Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse.
113
Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu.
114
Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu.
115
Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga.
116
Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika.
117
Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu.
118
Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake.
119
Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu.
120
Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu.
121
Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza.
122
Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze.
123
Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi.
124
Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
125
Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu.
126
Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu.
127
Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino.
128
Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.
129
Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse.
130
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
131
Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu.
132
Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani.
133
Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira.
134
Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu.
135
Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu.
136
Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu.
137
Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama.
138
Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu.
139
Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu.
140
Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda.
141
Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu.
142
Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona.
143
Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa.
144
Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo.
145
Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu.
146
Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu.
147
Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu.
148
Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu.
149
Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu.
150
Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu.
151
Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona.
152
Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya.
153
Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu.
154
Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja.
155
Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu.
156
Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu.
157
Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu.
158
Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu.
159
Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika
160
mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya.
161
Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu.
162
Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri.
163
Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu.
164
Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama.
165
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
166
Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu.
167
Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse.
168
Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona.
169
Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja.
170
Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu.
171
Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu.
172
Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.
173
Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu.
174
Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa.
175
Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza.
176
Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.
← Chapter 118
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 67
Chapter 68
Chapter 69
Chapter 70
Chapter 71
Chapter 72
Chapter 73
Chapter 74
Chapter 75
Chapter 76
Chapter 77
Chapter 78
Chapter 79
Chapter 80
Chapter 81
Chapter 82
Chapter 83
Chapter 84
Chapter 85
Chapter 86
Chapter 87
Chapter 88
Chapter 89
Chapter 90
Chapter 91
Chapter 92
Chapter 93
Chapter 94
Chapter 95
Chapter 96
Chapter 97
Chapter 98
Chapter 99
Chapter 100
Chapter 101
Chapter 102
Chapter 103
Chapter 104
Chapter 105
Chapter 106
Chapter 107
Chapter 108
Chapter 109
Chapter 110
Chapter 111
Chapter 112
Chapter 113
Chapter 114
Chapter 115
Chapter 116
Chapter 117
Chapter 118
Chapter 119
Chapter 120
Chapter 121
Chapter 122
Chapter 123
Chapter 124
Chapter 125
Chapter 126
Chapter 127
Chapter 128
Chapter 129
Chapter 130
Chapter 131
Chapter 132
Chapter 133
Chapter 134
Chapter 135
Chapter 136
Chapter 137
Chapter 138
Chapter 139
Chapter 140
Chapter 141
Chapter 142
Chapter 143
Chapter 144
Chapter 145
Chapter 146
Chapter 147
Chapter 148
Chapter 149
Chapter 150
Chapter 120 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
67
68
69
70
71
72
73
74
75
76
77
78
79
80
81
82
83
84
85
86
87
88
89
90
91
92
93
94
95
96
97
98
99
100
101
102
103
104
105
106
107
108
109
110
111
112
113
114
115
116
117
118
119
120
121
122
123
124
125
126
127
128
129
130
131
132
133
134
135
136
137
138
139
140
141
142
143
144
145
146
147
148
149
150