bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Psalms 89
Psalms 89
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 88
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 67
Chapter 68
Chapter 69
Chapter 70
Chapter 71
Chapter 72
Chapter 73
Chapter 74
Chapter 75
Chapter 76
Chapter 77
Chapter 78
Chapter 79
Chapter 80
Chapter 81
Chapter 82
Chapter 83
Chapter 84
Chapter 85
Chapter 86
Chapter 87
Chapter 88
Chapter 89
Chapter 90
Chapter 91
Chapter 92
Chapter 93
Chapter 94
Chapter 95
Chapter 96
Chapter 97
Chapter 98
Chapter 99
Chapter 100
Chapter 101
Chapter 102
Chapter 103
Chapter 104
Chapter 105
Chapter 106
Chapter 107
Chapter 108
Chapter 109
Chapter 110
Chapter 111
Chapter 112
Chapter 113
Chapter 114
Chapter 115
Chapter 116
Chapter 117
Chapter 118
Chapter 119
Chapter 120
Chapter 121
Chapter 122
Chapter 123
Chapter 124
Chapter 125
Chapter 126
Chapter 127
Chapter 128
Chapter 129
Chapter 130
Chapter 131
Chapter 132
Chapter 133
Chapter 134
Chapter 135
Chapter 136
Chapter 137
Chapter 138
Chapter 139
Chapter 140
Chapter 141
Chapter 142
Chapter 143
Chapter 144
Chapter 145
Chapter 146
Chapter 147
Chapter 148
Chapter 149
Chapter 150
Chapter 90 →
1
Inu Chauta, ndidzaimba mosalekeza nyimbo yotamanda chikondi chanu chosasinthika. Ndidzalalika ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.
2
Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya, kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
3
Inu mwanena kuti, “Ndachita chipangano ndi wosankhidwa wanga, ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,
4
‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya, ndidzasungira mibadwo yonse mpando wako waufumu.’ ”
5
Zakumwamba zimatamanda zodabwitsa zanu, Inu Chauta, zimatamanda kukhulupirika kwanu mu msonkhano wa oyera mtima.
6
Kodi ndani mu mlengalenga angathe kulingana ndi Chauta? Ndani pakati pa akumwamba amafanafana naye?
7
Mulungu ndiye amene amamuwopa mu msonkhano wa anthu oyera mtima, ndiye wamkulu ndi wolemekezeka pakati pa onse omzungulira.
8
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta, amene muli okhulupirika pa zonse?
9
Mumalamulira nyanja yaukali. Mafunde ake akakwera, Inu mumaŵakhalitsa bata.
10
Mudatswanya chilombo cha m'nyanja ndi kuchisandutsa mtembo. Mudabalalitsa adani anu ndi mkono wanu wamphamvu.
11
Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.
12
Mudalenga kumpoto ndi kumwera. Mapiri a Tabori ndi Heremoni akukutamandani ndi chimwemwe.
13
Inu muli ndi mphamvu zonse. Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
14
Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita.
15
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
16
Iwowo amakondwa masiku onse chifukwa cha Inu, ndipo amatamanda kulungama kwanu.
17
Amanyadira ulemerero wanu ndi mphamvu zanu. Mphamvu zathu zalimba chifukwa mwatikomera mtima.
18
Chauta ndiye chishango chathu, Woyera wa Israele ndiye mfumu yathu.
19
Kale mudalankhula m'masomphenya kwa anthu anu okhulupirika, mudati, “Ndamuveka chisoti chaufumu munthu amene ali wamphamvu, ndamukweza amene ali wosankhidwa pakati pa anthu.
20
“Ndampeza Davide mtumiki wanga, ndamdzoza ndi mafuta anga oyera,
21
“Kotero kuti dzanja langa lidzamchirikiza mpaka muyaya, mkono wanganso udzamulimbitsa.
22
“Adani sadzampambana, anthu oipa sadzamtsitsa.
23
Ndidzatswanya adani ake pamaso pake, ndi kukantha odana naye.
24
“Kukhulupirika ndiponso chikondi changa chosasinthika zidzakhala naye, ndidzalimbitsa mphamvu zake, kuti mbiri yanga isungike.
25
Ndidzakuza ufumu wake kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kukafika ku mtsinje wa Yufurate.
26
“Iye adzandiwuza kuti, ‘Inu ndinu Atate anga, Mulungu wanga, Thanthwe londipulumutsa.’
27
Ndithu ndidzamsandutsa mwana wanga wachisamba, adzakhala wopambana mafumu a dziko lapansi.
28
“Ndidzamkonda nthaŵi zonse ndi chikondi changa chosasinthika, chipangano changa ndi iye sichidzaphwanyika.
29
Ndidzakhazikitsa zidzukulu zake pa mpando wachifumu, mpaka muyaya, ndipo ufumu wake udzakhala waukulu ngati mlengalenga.
30
“Koma ngati ana ake asiya lamulo langa, ndipo satsata malangizo anga,
31
ngati aphwanya malamulo anga, ndipo sasunga malangizo anga,
32
“ndidzaŵalanga ndi ndodo, chifukwa cha zolakwa zao, ndidzaŵakwapula ndi zikoti chifukwa cha machimo ao.
33
Koma Davide sindidzamchotsera chikondi changa chosasinthika, sindidzakhala wosakhulupirika kwa iye.
34
“Sindidzaswa chipangano changa, kapena kusintha mau otuluka pakamwa panga.
35
Ndidalumbira kamodzinkamodzi kuti, ‘Pali dzina langa loyera! Sindidzamnamiza Davide.’
36
“Zidzukulu zake sizidzatha mpaka muyaya, mpando wake wachifumu udzakhalapo nthaŵi zonse, monga m'mene likhalira dzuŵa pamaso panga.
37
Ufumu wake udzakhazikika mpaka muyaya ngati mwezi, mboni yanga yokhulupirika mu mlengalenga.”
38
Koma tsopano Inu mwamtaya ndi kumkana wodzozedwa wanu, mwamkwiyira kwambiri.
39
Mwakana chipangano chanu ndi mtumiki wanu, mwadetsa m'fumbi chisoti chake chaufumu.
40
Mwagumula makoma ake onse, mwasandutsa malinga ake mabwinja.
41
Onse odutsa amamlanda zinthu zake, anzake amamunyodola.
42
Mwalimbikitsa amaliwongo ake, mwakondwetsa adani ake onse.
43
Inde, mwabunthitsa lupanga lake, ndipo simudamlimbitse pa nkhondo.
44
Mwamchotsera ndodo yachifumu m'manja, ndipo mwataya pansi mpando wake wachifumu.
45
Mwamkalambitsa msanga, mwamkuta ndi manyazi.
46
Kodi mpaka liti, Inu Chauta? Kodi mudzandibisalira mpaka muyaya?
47
Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa. Zoonadi, mudalenga anthu onse kuti akhale a moyo waufupi kwambiri.
48
Kodi ndani angathe kukhala moyo osaona imfa? Ndani angathe kupulumutsa moyo wake polewa mphamvu za malo a anthu akufa?
49
Ambuye, chili kuti chikondi chanu chosasinthika chakale chija, chimene mudachilumbirira Davide kuti mudzakhala wokhulupirika?
50
Ambuye, kumbukirani kunyozedwa kwa mtumiki wanune, ndakhala ndikupirira chamumtima chipongwe cha anthu.
51
Kumbukirani kuti amene akundinyozawo ndi adani anu, Inu Chauta, iwo akunyoza Wodzozedwa wanu paliponse pamene waponda.
52
Chauta atamandike mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo.
← Chapter 88
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 67
Chapter 68
Chapter 69
Chapter 70
Chapter 71
Chapter 72
Chapter 73
Chapter 74
Chapter 75
Chapter 76
Chapter 77
Chapter 78
Chapter 79
Chapter 80
Chapter 81
Chapter 82
Chapter 83
Chapter 84
Chapter 85
Chapter 86
Chapter 87
Chapter 88
Chapter 89
Chapter 90
Chapter 91
Chapter 92
Chapter 93
Chapter 94
Chapter 95
Chapter 96
Chapter 97
Chapter 98
Chapter 99
Chapter 100
Chapter 101
Chapter 102
Chapter 103
Chapter 104
Chapter 105
Chapter 106
Chapter 107
Chapter 108
Chapter 109
Chapter 110
Chapter 111
Chapter 112
Chapter 113
Chapter 114
Chapter 115
Chapter 116
Chapter 117
Chapter 118
Chapter 119
Chapter 120
Chapter 121
Chapter 122
Chapter 123
Chapter 124
Chapter 125
Chapter 126
Chapter 127
Chapter 128
Chapter 129
Chapter 130
Chapter 131
Chapter 132
Chapter 133
Chapter 134
Chapter 135
Chapter 136
Chapter 137
Chapter 138
Chapter 139
Chapter 140
Chapter 141
Chapter 142
Chapter 143
Chapter 144
Chapter 145
Chapter 146
Chapter 147
Chapter 148
Chapter 149
Chapter 150
Chapter 90 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
67
68
69
70
71
72
73
74
75
76
77
78
79
80
81
82
83
84
85
86
87
88
89
90
91
92
93
94
95
96
97
98
99
100
101
102
103
104
105
106
107
108
109
110
111
112
113
114
115
116
117
118
119
120
121
122
123
124
125
126
127
128
129
130
131
132
133
134
135
136
137
138
139
140
141
142
143
144
145
146
147
148
149
150