bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ezekiel 17
Ezekiel 17
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 18 →
1
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, ipha mwambi, nunene fanizo kwa nyumba ya Israyeli,
3
nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ciombankhanga cacikuru ndi mapiko akuru, ndi maphiphi atali, odzala nthenga ca mathotho-mathotho, cinafika ku Lebano, nicitenga nsonga ya mkungudza,
4
cinabudula nsonga yosomphoka ya nthambi zace zanthete, ndi kumuka nayo ku dziko la malonda, cinaiika m'mudzi wa amalonda.
5
Cinatengakonso mbeu ya m'dziko, ndi kuibzala m'nthaka yokoma, cinaiika panali madzi ambiri, cinaioka ngati mtengo wamsondodzi.
6
Ndipo inaphuka, nikhala mpesa wotambalala wofupi msinkhu, nthambi zace zinapindikira momwe, ndi mizu yace pansi pace, nikhala mpesa, nuonetsa nthambi ndi kuphuka mphukira.
7
Panalinso ciombankhanga cina cacikuru, ndi mapiko akuru, ndi nthenga zambiri; ndipo taona, mpesa uwu unacipindira mizu yace, nucilunjikitsira nthambi zace, kucokera pookedwa pace, kuti ciuthirire madzi.
8
Unaokedwa mu nthaka yabwino kuli madzi ambiri, kuti uphuke nthambi, nubale zipatso, nukhale mpesa wabwino.
9
Uziti, Atero Ambuye Yehova, Udzakondwa kodi? sadzausula ndi kudula zipatso zace, kuti uume, kuti masamba ace onse ophuka aume, ngakhale palibe mphamvu yaikuru, kapena anthu ambiri akuuzula?
10
Inde ungakhale waokedwa udzakondwa kodi? sudzauma ciumire kodi pakuuomba mphepo ya kum'mawa? udzauma pookedwa apo udaphuka.
11
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti.
12
Uziti tsono kwa nyumba ya mpandukoyi, Simudziwa kodi izi nciani? Uziti, Taonani mfumu ya ku Babulo inadza ku Yerusalemu, nitenga mfumu yace ndi akalonga ace, nibwera nao kuti iye ku Babulo;
13
nitenga wa mbumba yacifumu, nicita naye pangano, nimlumbiritsa, nicotsa amphamvu a m'dziko;
14
kuti ufumuwo ukhale wopepuka, kuti usadzikweze, koma kuti pakusunga pangano lace ukhale.
15
Koma anapandukira ndi kutuma mithenga yace ku Aigupto, kuti ampatse akavalo ndi anthu ambiri. Adzapindula kodi? adzapulumuka wakucita izi? atyole pangano ndi kupulumuka kodi?
16
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, pamalo pokhala mfumu, imene idamcititsa ufumu, imene anapeputsa lumbiro lace, imene anatyola pangano lace, adzafa pamodzi ndi iye pakati pa Babulo.
17
Ndipo Farao ndi nkhondo yace yaikuru, ndi khamu lace launyinji, sadzacita pamodzi naye kunkhondo, pakuunda mtumbira, ndi kumanga malinga, kulikha anthu ambiri.
18
Pakuti anapepula lumbiro, ndi kutyola pangano, angakhale anapereka dzanja lace; popeza anacita izi zonse sadzapulumuka.
19
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Pali Ine, lumbiro langa, analipepula, ndi pangano langa analityola, ndidzawabweza pamutu pace.
20
Ndidzamphimbanso ndi ukonde wanga, nadzakodwa iye mu msampha wanga; ndipo ndidzadza naye ku Babulo, ndi kunena naye komweko mlandu wa kulakwa kwace anandilakwira nako.
21
Ndipo othawa ace onse m'magulu ace onse adzagwa ndi lupanga, ndi otsala adzabalalitsidwa ku mphepo zonse; ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndanena.
22
Atero Ambuye Yehova, Ndidzatenganso nsonga ya mkungudza wautali ndi kulika; ndidzabudula nsonga yosomphoka'ya nthambi zace zanthete, ndi kuioka pa phiri lalitali lothubvuka;
23
pa phiri lothubvuka la Israyeli ndidzaioka, ndipo idzaphuka nthambi ndi kubala zipatso, nidzakhala mkungudza wokoma, ndi m'munsi mwace mudzakhala mbalame ziri zonse za mapiko ali onse; mu mthunzi wa nthambi zace zidzabindikira.
24
Ndipo mitengo yonse ya kuthengo idzadziwa kuti Ine Yehova ndatsitsa mtengo wosomphoka, ndakuza mtengo waung'ono, ndaumitsa mtengo wauwisi, ndi kuphukitsa mtengo wouma; Ine Yehova ndanena ndi kucicita.
← Chapter 16
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 18 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48