bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ezekiel 18
Ezekiel 18
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 19 →
1
Ndipo anandidzera mau a Yehoya, akuti,
2
Mutani inu ndi kunena mwambi uwu za dziko la Israyeli, wakuti, Atate adadya mphesa zosacha, ndi mano a ana ayayamira.
3
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, simudzaonanso cifukwa ca kunena mwambiwu m'Israyeli.
4
Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wocimwawo ndiwo udzafa.
5
Koma munthu akakhala wolungama, nakacita ciweruzo ndi cilungamo,
6
wosadya pamapiripo, wosakweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace, kapena kuyandikira mkazi ataoloka,
7
wosasautsa munthu ali yense, koma wambwezera wangongole cigwiriro cace, wosatenga zofunkha, anampatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,
8
wosapereka molira phindu, wosatenga coonjezerapo wobweza dzanja lace lisacite cosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzace,
9
amayenda m'malemba anga, nasunga maweruzo anga kucita cokhulupirika; iye ndiye wolungama, adzakhala ndi moyo ndithu, anena Ambuye Yehova.
10
Akabala mwana ndiye mkhungu, wokhetsa mwazi, wocita cimodzi ca izi,
11
wosacita zabwino zonse zija, koma anadyanso pamapiri, naipsa mkazi wa mnansi wace,
12
nasautsa osauka ndi osowa, natenga zofunkha, wosabwezera cigwiriro, nakweza maso ace kumafano, nacita conyansa,
13
napereka molira phindu, nalandira coonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? sadzakhala ndi moyo, anacita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, niwazi wace umkhalira.
14
Taona tsono, yemweyo akabala mwana uyu, naona zocimwa zonse adazicita atate wace, naopa wosacita zoterezo,
15
wosadya pamapiri, kapena kukweza maso ace ku mafano a nyumba ya Israyeli, wosaipsa mkazi wa mnansi wace,
16
kapena kusautsa wina ali yense, wosatenga cigwiriro, wosatenga zofunkha; koma anapatsa wanjala cakudya cace, nabveka wamarisece ndi cobvala,
17
naletsa dzanja lace pa wozunzika, wosalandira phindu kapena coonjezerapo, wocita maweruzo anga, nayenda m'malemba anga; uyu sadzafera mphulupulu ya atate wace, adzakhala ndi moyo ndithu.
18
Atate wace, popeza anazunza cizunzire, nafunkha za mbale wace, nacita cimene siciri cabwino pakati pa anthu ace, taona, adzafa mu mphulupulu yace.
19
Koma inu mukuti, Alekeranji mwana kusenza mphulupulu za atate wace? Mwanayo akacita ciweruzo ndi cilungamo, nakasunga malemba anga onse, ndi kuwacita, adzakhala ndi moyo ndithu.
20
Moyo wocimwawo ndiwo udzafa; mwana sadzasenza mphulupulu zaatate wace, ndi atate sadzasenza mphulupulu za mwana; cilungamo ca wolungama cidzamkhalira, ndi coipa ca woipa cidzamkhalira,
21
Koma woipayo akabwerera kusiya macimo ace onse adawacita nakasunga malemba anga onse, ndi kucita ciweruzo ndi cilungamo, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
22
Nnena cimodzi conse ca zolakwa zace zonse adazicita cidzakumbukika cimtsutse; m'cilungamo cace adacicita adakhala ndi moyo.
23
Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yace, ndi kukhala ndi moyo?
24
Koma wolungamayo akabwerera kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, ndi kucita monga mwa zonyansa zonse azicita woipa, adzakhala ndi moyo kodi? Nnena cimodzi ca zolungama zace zonse adzazicita cidzakumbukika m'kulakwa kwace analakwa nako, ndi m'kucimwa kwace anacimwa nako; momwemo adzafa.
25
Koma mukuti, Njira ya Ambuye njosayenera. Tamvera tsono nyumba ya Israyeli, Kodi njira yanga njosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?
26
Wolungamayo akatembenukira kuleka cilungamo cace, nakacita mphulupulu, adzafa momwemo; m'mphulupulu yace adaicita adzafa.
27
Ndipo woipayo akatembenukira kuleka coipa cace adacicita, nakacita ciweruzo ndi cilungamo, adzapulumutsa moyo wace.
28
Popeza anasamalira, natembenukira kuleka zolakwa zace zonse adazicita, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.
29
Koma nyumba ya Israyeli imanena, Njira ya Ambuye njosayenera, Inu, nyumba ya Israyeli, kodi njira zanga nzosayenera? njira zanu si ndizo zosayenera?
30
Cifukwa cace ndidzakuweruzani inu, nyumba ya Israyeli, yense monga mwa njira zace, ati Ambuye Yehova. Bwererani, nimutembenukire kuleka zolakwa zanu zonse, ndipo simudzakhumudwa nazo, ndi kuonongeka nayo mphulupulu.
31
Tayani, ndi kudzicotsera zolakwa zanu zonse zimene munalakwa nazo, ndi kudzifunira mtima watsopano, ndi mzimu watsopano; pakuti mudzaferanji inu, nyumba ya Israyeli?
32
Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; cifukwa cace bwererani, nimukhale ndi moyo.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48