bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ezekiel 7
Ezekiel 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 8 →
1
Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
2
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, atero Ambuye Yehova kwa dziko la Israyeli, Kwatha; kwafika kutha kwace pa ngondya zinai za dziko.
3
Tsopano kwakudzera kutha kwako, ndipo ndidzakutumizira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zanse.
4
Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzacita cifundo, koma ndidzakubwezera njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
5
Atero Yehova Mulungu, Coipa, coipa ca pa cokha, taona cirinkudza.
6
Kutha kwafika, kwafika kutha, kwakugalamukira, taona kwafika.
7
Tsoka lako lakufikira, nzika iwe, yafika nthawi, tsiku liri pafupi, ndilo laphokoso, si lakupfuula mokondwera kumapiri,
8
Katsala kamphindi, ndipo ndidzakutsanulira ukali wanga, ndi kukukwaniritsira mkwiyo wanga, ndi kukuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse.
9
Ndipo diso langa silidzalekerera, wosacita cifundo Ine, ndidzakubwezera monga mwa njira zako, ndi zonyansa zako zidzakhala pakati pako; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakukantha.
10
Taona, tsikuli, taona, lafika; tsoka lako laturuka, ndodo yaphuka mphundu za maluwa, kudzitama kwaphuka.
11
Ciwawa cauka cikhale ndodo ya coipa; sadzawatsalira ndi mmodzi yense, kapena wa unyinji wao, kapena wa cuma cao; sipadzakhalanso kuwalira maliro.
12
Yafika nthawi, layandikira tsikulo, wogula asakondwere, ndi wogulitsa asamve cisoni; pakuti mkwiyo ukhalira unyinji wao wense.
13
Pakuti wogulitsa sadzabwera ku cogulitsaco, cinkana akali ndi moyo, popeza masomphenyawo akunena unyinji wace wonse sadzapita pacabe, ndipo palibe mmodzi adzalimbitsa moyo wace m'mphulupulu yace.
14
Aomba lipenga, nakonzeratu zonse, koma palibe womuka kunkhondo; pakuti mkwiyo wanga ukhalira unyinji wace wonse.
15
Kunja kuli lupanga, ndi m'katimo muli mliri ndi njala; wokhala kuthenso adzafa ndi lupanga, ndi wokhala m'mudziyo njala ndi mliri zidzamutha.
16
Ndipo akupulumuka mwa iwo adzapulumuka, koma adzakhala kumapiri ngati njiwa za kuzigwa, onse akubuula, ali yense m'mphulupulu zace.
17
Manja onse adzalenda, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi.
18
Ndipo adzadzimangira m'cuuno ndi ziguduli, ndi zoopsetsa zidzawaphimba, ndi nkhope zonse zidzacita manyazi, ndi mitu yao yonse idzacita dazi.
19
Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golidi wao cinthu codetsedwa; siliva wao ndi golidi wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi cokhumudwitsa ca mphulupulu zao.
20
Ndipo cokometsera cace cokongola anaciyesa codzikuza naco, napanga naco mafanizo ao onyansa, ndi zonyansa zao zina; cifukwa cace ndinapatsa ici cikhale cowadetsa.
21
Ndipo ndidzacipereka m'dzanja la alendo cikhale colandika, ndi kwa oipa a m'dziko cikhale cofunkha; ndipo adzaciipsa.
22
Ndipo nkhope yanga idzawayang'anira kumbali, ndipo iwo adzadetsa pobisika panga, nadzalowamo acifwamba, nadzamudetsa.
23
Sula unyolo, popeza dziko ladzala ndi mirandu yamwazi, ndi mudzi wadzala ndi ciwawa.
24
Cifukwa cace ndidzabwera nao amitundu oipitsitsa, ndipo iwo adzalandira nyumba zao ngati colowa, ndidzaleketsanso kudzikuza kwa amphamvu, kuti adetsedwe malo ao opatulika.
25
Cionongeko cirinkudza, adzafunafuna mtendere, koma palibe.
26
Lidzafika tsoka lotsatana-tsatana, kudzakhalanso mbiri yotsatana-tsatana, ndipo adzafunafuna masomphenya a mneneri, koma malamulo adzatayikira wansembe, uphungu ndi kutayikira akulu.
27
Mfumu idzalira maliro, ndi kalonga adzabvala cipasuko, ndi manja a anthu a m'dziko adzanjenjemera, Ndidzawacitira monga mwa njira zao, ndi kuwaweruza monga mwa maweruzo ao; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48