bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ezekiel 21
Ezekiel 21
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 22 →
1
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israyeli kulitsutsa;
3
nuziti kwa dziko la Israyeli, Atero Yehova, Taona Ine ndine wotsutsana nawe, ndidzasolola lupanga langa m'cimace, ndi kukulikhira olungama ndi oipa.
4
Popeza ndidzakulikhira olungama ndi oipa, cifukwa cace lupanga langa lidzasololokera anthu onse, kuyambira kumwera kufikira kumpoto;
5
ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupangalanga m'cimace, silidzabwereranso.
6
Koma wobadwa ndi munthu iwe, usa moyo, ndi kuduka msana, ndi kuwawa mtima, uuse moyo pamaso pao.
7
Ndipo kudzakhala akanena ndi iwe, Uusa moyo cifukwa ninji? uzikati, Cifukwa ca mbiri; pakuti ikudza, ndi mtima uli wonse udzasungunuka, ndi manja onse adzalenda, ndi mzimu uli wonse udzakomoka, ndi maondo onse adzaweyeseka ngati madzi; taona irinkudza, inde idzacitika, ati Ambuye Yehova.
8
Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,
9
Wobadwa ndi munthu iwe, nenera ndi kuti, Atero Yehova, Nena, Lupanga, lupanga lanoledwa, latuulidwanso;
10
lanoledwa kuti liphetu, lituulidwa kuti linge mphezi; tisekererepo kodi? ndilo ndodo yacifumu ya mwana wanga, yopeputsa mtengo uli wonse.
11
Ndipo analipereka alituule, kuti acite nalo lupangali analinola, inde analituula kulipereka m'dzanja la wakupha.
12
Pfuula ndi kulira, wobadwa ndi munthu iwe, pakuti likhalira pa anthu anga, likhalira pa akalonga onse a Israyeli, laperekedwa kulupanga pamodzi ndi anthu anga; cifukwa cace panda pancafu pako.
13
Pakuti pali kuyesedwa; ndipo nanga ndodo yacifumu yopeputsa ikapanda kukhalanso? ati Ambuye Yehova.
14
Ndipo wobadwa ndi munthu iwe, nenera, nuombe manja, lupanga lipitirize katatu, lupanga la wolasidwa ndilo lupanga la wolasidwa wamkuruyo, limene liwazinga.
15
Ndalozetsa nsonga ya lupanga ku zipata zao zonse, kuti mtima wao usungunuke, ndi kukhumudwa kwao kucuruke; ha! analituula linyezimire, analisongoza liphe,
16
Udzisonkhanitsire pamodzi, muka ku dzanja lamanja; undandalitsa nkhondo kumuka kulamanzere; kuli konse ilozako nkhope yako.
17
Inenso ndidzaomba manja anga, ndipo ndidzakukwaniritsa ukali wanga; Ine Yehova ndanena.
18
Ndipo mau a Yehova anandidzera, akuti,
19
Wobadwa ndi munthu iwe, udziikire njira ziwiri zodzera lupanga la mfumu ya ku Babulo; zonse ziwiri zicokere dziko lomwelo; nulembe cizindikilo colozera, ucilembe pa mphambano ya njira ya kumudzi.
20
Uiike njira yodzera lupanga kumka ku Raba wa ana a Amoni, ndi ya ku Yuda ku Yerusalemu, mudzi walinga.
21
Pakuti mfumu ya ku Babulo aima pa mphambano ya njira, polekana njira ziwirizo, kuti aombeze maula; agwedeza mibvi, afunsira kwa aterafi, apenda ndi ciwindi.
22
M'dzanja lace lamanja muli ula wa ku Yerusalemu, kuika zogundira, kutsegula pakamwa pa kupha, kukweza mau ndi kupfuula, kuikira zitseko zogundira, kuundira mtumbira, kumanga malinga.
23
Ndipo kudzakhala ngati kuombeza konyenga pamaso pa iwo amene anawalumbirira malumbiro; koma akumbutsa mphulupulu kuti akodwe.
24
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mwakumbutsa mphulupulu yanu pobvumbuluka zolakwa zanu, kotero kuti macimo anu aoneka m'zonse muzicita, popeza mukumbukika, mudzagwidwa ndi dzanja.
25
Ndipo iwe wolasidwa woipa, kalonga wa Israyeli, amene lafika tsiku lako, nthawi ya mphulupulu yotsiriza;
26
atero Ambuye Yehova, Cotsa cilemba, bvula korona, ufumu sudzakhalanso momwemo, kweza copepuka, cepsa cokwezeka.
27
Ndidzagubuduza gubuduza gubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini ciweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.
28
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nenera, nuziti, Atero Ambuye Yehova za ana a Amoni, ndi za citonzo cao; nuziti, Lupanga, lupanga lasololedwa, latuulidwa, kuti likaphe, kuti liononge, likhale lonyezimira.
29
Akuonera zopanda pace, akuombezera mabodza, lupanga likugoneka pa makosi a oipa olasidwa, amene lafika tsiku lao nthawi ya mphulupulu yotsiriza.
30
Ulibwezere m'cimace. Pamalo unalengedwapo m'dziko la kubadwa kwako ndidzakuweruza.
31
Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.
32
Udzakhala ngati nkhuni ya pamoto, mwazi wako udzakhala pakati pa dziko, sudzakumbukikanso; pakuti Ine ndine Yehova ndacinena.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48