bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Ezekiel 31
Ezekiel 31
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
1
Ndipo kunali caka cakhumi ndi cimodzi, mwezi wacitatu, tsiku loyamba la mwezi, anandidzera mau a Yehova, akuti,
2
Wobadwa ndi munthu iwe, nena kwa Farao mfumu ya Aigupto ndi aunyinji ace, Ufanana ndi yani m'ukulu wako?
3
Taona, Asuri anali mkungudza wa ku Lebano ndi nthambi zokoma zobvalira, wautali msinkhu, kunsonga kwace ndi kumitambo.
4
Madzi anaumeretsa, cigumula cinaukulitsa, mitsinje yace inayenda, nizungulira munda wace, nipititsa micera yace ku mitengo yonse ya kuthengoko.
5
Cifukwa cace msinkhu wace unaposa mitengo yonse ya kuthengo, ndi nthambi zace zinacuruka, ndi nthawi zace zinatalika, Cifukwa ca madzi ambiri pophuka uwu.
6
Mbalame zonse za m'mlengalenga zinamanga zisa zao pa nthambi zace, ndi pansi pa nthawi zace zinaswana nyama zonse za kuthengo, ndi pa mthunzi wace inakhala mitundu yonse yaikuru ya anthu.
7
M'mwemo unakoma m'ukulu wace, m'kutalika kwa nthawi zace, popeza muzu wace unakhala ku madzi ambiri.
8
Mikungudza ya m'munda wa Mulungu siinathe kuubisa, milombwasimanga nthambi zace, mifula siinanga nthawi zace; m'munda wa Mulungu munalibe mtengo wofanana nao kukoma kwace.
9
Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zace zocuruka; ndi mitengo yonse ya m'Edene inali m'munda wa Mulungu inacita nao nsanje.
10
Cifukwa cace atero Ambuye Yehova, Popeza mtengowo unakuza msinkhu wace, nufikitsa nsonga yace kumitambo, nukwezeka mtima wace m'kukula kwace,
11
ndidzaupereka m'dzanja la wamphamvu wa amitundu; iye adzacita naotu, Ine ndautaya mwa coipa cace.
12
Ndipo alendo oopsawo a amitundu anaulikhatu, nausiya; nthawi zace zidagwa pamapiri ndi m'zigwa zonse, ndi nthambi zace zinatyokera ku timitsinje tonse ta m'dziko; ndi mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi inatsika ku mthunzi wace, niusiya.
13
Pogwera pace padzakhala mbalame zonse za m'mlengalenga, ndi nyama zonse za kuthengo zidzakhala pa nthambi zace;
14
kuti mitengo iri yonse ya kumadzi isadzikuze cifukwa ca msinkhu wao, kapena kufikitsa nsonga zao pakati pa mitambo, ndi kuti amphamvu ao asaime m'kukula kwao, ndiwo onse akumwa madzi; pakuti onsewo aperekedwa ku imfa munsi mwace mwa dziko, pakati pa ana a anthu, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda.
15
Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinacititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinacepsa mitsinje yace, ndi madzi akuru analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebano, ndi mitengo yonse ya kuthengo inafota cifukwa ca uwo.
16
Ndirtagwedeza amitundu ndi phokoso la kugwa kwace, muja ndinamgwetsera kumanda, pamodzi ndi iwo otsikira kumanda; ndi mitengo yonse ya ku Edene yosankhika, ndi yokometsetsa ya ku Lebano, yonse yakumwa madzi, inasangalala munsi mwace mwa dziko lapansi.
17
Iwonso anatsika naye kumanda kwa iwo ophedwa ndi lupanga, ndiwo amene adakhala dzanja lace okhala mumthunzi mwace pakati pa amitundu.
18
Momwemo ufanana ndi yani m'ulemerero ndi ukulu pakati pa mitengo ya Edene? koma udzatsitsidwa pamodzi ndi mitengo ya Edene munsi mwace mwa dziko lapansi, udzagona pakati pa osaditiidwa, pamodzi ndi iwo ophedwa ndi lupanga. Uwu ndi Farao ndi aunyinji ace onse, ati Ambuye Yehova.
← Chapter 30
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 32 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48