bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Isaiah 33
Isaiah 33
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 34 →
1
Tsoka kwa iwe amene usakaza, cinkana sunasakazidwa; nupangira ciwembu, cinkana sanakupangira iwe ciwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira ciwembu, iwo adzakupangira iwe ciwembu.
2
Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira Inu; mukhale dzanja lathu m'mawa ndi m'mawa, cipulumutso cathunso m'nthawi ya mabvuto.
3
Pa mau a phokoso mitundu ya anthu yathawa; ponyamuka iwe amitundu abalalika,
4
Ndipo zofunkha zanu zidzasonkhanitsidwa, monga ziwala zisonkhana; monga madzombe atumpha, iwo adzatumpha pa izo.
5
Yehova wakwezedwa; pakuti akhala kumwamba; Iye wadzaza Ziyoni ndi ciweruzo ndi cilungamo.
6
Ndipo kudzakhala cilimbiko m'nthawi zako, cipulumutso cambiri, nzeru ndi kudziwa; kuopa kwa Yehova ndiko cumacace.
7
Taonani, olimba mtima ao angopfuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.
8
Njira zamakwalala zikufa, kulibe woyendamo; Asuri watyola cipangano, wanyoza midzi, sasamalira anthu.
9
Dziko lilira maliro ndi kulefuka; Lebano ali ndi manyazi, nafota; Saroni afanana ndi cipululu; pa Basana ndi Karimeli papukutika.
10
Tsopano ndidzauka, ati Yehova; tsopano ndidzanyamuka, tsopano ndidzakwezedwa.
11
Inu mudzatenga pakati ndi mungu, mudzabala ziputu; mpweya wanu ndi moto umene udzakumarizani inu.
12
Ndipo mitundu ya anthu idzanga potentha miyala yanjeresa; monga minga yodulidwa, nitenthedwa ndi moto.
13
Imvani inu amene muli kutari, cimene ndacita ndi inuamene muli pafupi, bvomerezani mphamvu zanga,
14
Ocimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto Wakunyeketsa? ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zacikhalire?
15
Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;
16
iye adzakhala pamsanje; malo ace ocinjikiza adzakhala malinga amiyala; cakudya cace cidzapatsidwa kwa iye; madzi ace adzakhala cikhalire.
17
Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwace; iwo adzaona dziko lakutari.
18
Mtima wako udzaganizira zoopsya; mlembi ali kuti? ali kuti iye amene anayesa msonkho? ali kuti iye amene anawerenga nsanja?
19
Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilume lacibwibwi, limene iwe sungalimve.
20
Tayang'ana pa Ziyoni, mudzi wa mapwando athu; maso ako adzaona Yerusalemu malo a phe, cihema cimene sicidzasunthidwa, ziciri zace sizidzazulidwa konse, zingwe zace sizidzadulidwa.
21
Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife m'cifumu, malo a nyanja zacitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikuru sizidzapita pamenepo.
22
Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.
23
Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wace, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo colanda cacikulu, cofunkha cinagawanidwa; wopunduka nafumfula.
24
Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.
← Chapter 32
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 34 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66